Aphunzitsi tigwirane manja potukula Maphunziro- Matchaya.

Bwana mkhubwa wa boma la Nsanje, Dr Medson Matchaya, wapempha aphunzitsi mbomali kuti achilimike pa ntchito zawo ndi cholinga chofuna kuonetsetsa kuti ophunzira akuchuta bwino pamayeso awo aboma.

Dr Matchaya amalankhula izi pomwe amatsekera mkumano wa masiku atatu omwe anachititsa mkati kati mwa sabatayi ndi akulu akulu aku nthambi ya maphunziro mbomali.

Mmawu ake Matchaya anati ndi okhumudwa ndi mmene boma la Nsanje lachitira pamayeso a standard 8 komanso folomu 2 mu zaka ziwiri zapitazi ndipo anachita changu potsindika kuti izi zikhala mbiri yakale.

” Taonani boma la Nsanje tili ndi mwayi, ine ngati DC ndimachokera mboma la Nsanje, mkulu wa zamaphunziro, a Greystone Alindiamwo, amachokeranso mboma lino, nanga zinthu zikuvuta pati?” Anadzifunsa motere Dr Matchaya,uku akupukusa mutu, kutsindika kuti izi zikhala mbiri tsopano.

Pamenepa Bwana mkhubwayu anati iye pamodzi ndi akulu akulu a zamaphunziro mboma la Nsanje aika ndondomeko zingapo zofuna kuonentsetsa kuti maphunziro mbomali akubwelera mchimake.

Poyambilira Matchaya apempha akulu akulu a zamaphunziro mbomali mothandizana ndi akulu akulu aku likulu la za maphunziro ku Lilongwe kuti akhale pa ntchito yoyendera aphunzitsi onse kuti aonetsetse ngati aphunzitsi akugwiradi ntchito zawo moyenera. Ndipo iye anatsindika kuti ntchitoyi ikayamba sabata la mmawali, iye adzakhala nawo pa mdipitiwo.

Mfundo ina ndiyofuna kulimbikitsa aphunzitsi komanso ophunzira omwe achita bwino pamayeso a standard 8,folomu 2 ndi 4 pomawapatsa mphoto zosiyana siyana.

Malingana ndi Matchaya, izi ziyamba chaka chino pamayeso omwe adutsawa ndipo zizachitika mkati kati mwa mwezi wa Disembala pomwe ophunzira omwe achita bwino ndi aphunzitsi omwe akhozetsa bwino pamaphunziro awo azakhale akulandira mphoto pamwambo omwe uzachitikire ku sukulu ya sekondale ya Nsanje.

Zambiri tikupatsirani pa avantmalawi.com

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *