Lero pa 12 April, 2021 ndi pamene bwalo loweluza milandu ya anthu olemba ndi ogwira ntchito ku Lilongwe likuyembekezera kumva mulandu omwe boma likufuna kutenga Chiletso chokaniza amphunzitsi kupitilira kunyanyala ntchito.
Aphunzitsi ochuluka mdziko Muno ali Kakasi kudikira Chikalata Chochokera ku Bungwe loyang’anira aphunzitsi -TUM, kuwavomereza kuti abwerere ku Ntchito kapena ayi.
Ngakhale mpaka lero Bungweli silinamasule aphunzitsi kupitiliza ntchito, ndikokayikitsa ngati tsiku lalero Maphunziro apilire popeza Unduna wa Zamaphunziro Kudzera m’maboma (DEM) osiyana siyana sudayale dondomeko zimene aphunzitsi akuyenera kutenga Pamene Nkhani ili ku Khothi.
Aphunzitsi ochuluka asonyeza kuti abwerera malo awo a Ntchito lero kukangomva zotsatira zochoka ku District Education Managers (DEM) Pamene boma linangowophyseza pamasamba a Mchezo kuti lidula malipiro kwa aphunzitsi amene sakalembetsa ku Ntchito lero.
Komabe ngakhale zili chomwechi, Undunawo sudalembe chibaluwa chodziwitsa a Mphunzitsi awo za Nkhaniyi.
Kodi nyengo ya makono ino, tizilankhulana Kudzera pa social media? Nanga Kodi ana anthu aziphunzira mmakomo mpaka liti?
avantmalawi.com