AMANGIDWA KAMBA KOSUNGA ANA KUJANDO

Anthu asanu ndi atatu amangidwa kumangochi kamba kotsekula jando nthawi ya sukulu.

Mneneri wa Polisi ya mangochi a Amina Tepani Daudi watsimikiza kuti anthuwa amangidwa usiku wa dzulo mmudzi mwanjombe mfumu yaikuku Chowe.

A Daudi ati mwa anthu omwe amangidwa ndi a mfumu yamudzimo, makolo a anawo komanso yemwe amayang’anira jandolo.
ndipo malingana ndi mneneri wapolisiyu ku jandoko kunali anyamata anayi azaka pakati pa zinayi ndi zisanu ndi chimodzi.

Apolisi amanga anthuwa kamba koti ndi mulandu kusunga ana kujando nthawi yamamphunziro ndipo izi zikusemphana ndi gawo 80 lamalamulo oyendetsera ufulu wa ana.

www.avantmalawi.com

DR MWALE

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *