lero masamba a mchezo monga Facebook komanso WhatsApp yazaza ndi Kanema yemwe akuonetsa alonda a kampani ina yotchuka mdziko muno ya G4S akumenya komanso kunzunza mnyamata wachichepere kamba koti anamupeza akuba zinthu.
Alondawa anamugwaditsa pa kileti ya mowa kwinaku akumumenya, koma chilangochi kwa Iwo sichinali chokwana ndipo anapitiliza kumumanga nyakula pogwilitsa ntchito Malaya ake ndikumuponya pa madzi pomwe anamulamula kuti azigudubuka.
Malingana ndi Avant publication yapeza kuti anduna azachitetezo ataonera kanemayi alamula kuti alondawa amangidwe. Ife tikhala tikutsatila nkhaniyi mwachidwi mpaka chilungamo chioneke.
Tiyamikire zomwe achita a chimwendo Banda kamba koonetsetsa kuti chilungamo chisakhotetsedwe
www.avantmalawi.com
*DR MWALE*