Apolisi m’boma la nkhatabay amanga a charles Mwamphachi kamba kopezeka ndi zipangizo zochuluka zoyezera malungo opanda chilolezo.
A Mwamphasi omwe ndi azaka 32 akukayikiridwa kuti akusunga zipangizo zokwana 2,000 zoyezera malungo mosavomerezeka.
Olankhulira a Police a Ku Nkhatabay a Kondwani James atitsimikizira avant publications kuti zmkuluyi wagwidwa pa Msika wa Sanga pomwe anthu akufuna kwabwino anatsina khutu apolisi pamene a Mwamphasi amachoka ku Dwangwa kupita ku boma la Nkhatabay ndipo zinali zoyikidwa muma katoni ndipo mu katoni iliyonse zinalimo 25.
Mchitidwe osunga kapena opezeka ndi zipangizo zachipatala ukuchulukira mdziko muno pomwe amalawi ambiri akuvutika mzipatala kusowa zipangizozi. Avant publications ikutsatira mwachidwi nkhaniyi ndipo tikupatsirani zambiri.
www.avantmalawi.com
DR MWALE