Panja pa nyumba ya Malamulo ku mmawa wa lero pa 14 February kuli achitetezo ochuluka pamene zokambilana zikupitilira mkati mwa Nyumbayi.
Lero ndi tsiku lachinayi pamene aphungu akhale akukambilana, ndipo aphungu ena 25 a DPP dzulo anachita m’bindikilo paja pa Nyumbayi pamene anakanizidwa kulowa mu Nyumba ya Malamulo kutsatira zisokonezo anachita mu nyumbayi.
Nawo achinyamata a Malawi Congress Party akhamukira pa manda a Maleme Hastings Kamuzu Banda ndi zogwirira ntchito monga zitchetcho komanso makasu.
Kulankhula ndi achinyamatawa akuti iwo akufuna akonze pamalopo komanso atetezepo pa phekesera imene amvetsedwa kuti chipani cha DPP chikufuna kulimbikitsa anthu za kalembera wa ziphaso za nzika.
Komabe chipanichi chatsindika kuti ulendo olimbikitsa anthuwa ozakhalapo lachisanu.
A Victor Musowa alankhula kuti aphungu chipanichi lero apitilira kuchita m’bindikiro panja pa Nyumba ya Malamulo.
Zambiri tsatani Avantmalawi.com