KUNALINJI MSABATAYI?

olemba Dr Mwale

Avant publications yakhala ikukupasirani nkhani zosiyanasiyana zomwe zachitika mdziko muno musabata yomwe ikuthayi. Ndipo nkutheka kuti enanu simunazitsate zonse koma Avant ikukumbutsani zomwe zinachitika.

*Kunje ndi mathanga sakulandira nawo malipiro*

Boma silinaikebe  ma komishonala awiri a chipani Cha DPP omwe ndi a jean mathanga komanso a kunje, kamba koti court linawapeza kuti sioyenera kukhala ma komishonala a bungwe la MEC. President Chakwera sanawapatse anthuwa makalata awo oti ndi ma komishonala a bungweli pomwe anzawo onse analandira kale ndipo Chakwera ananenetsa kuti sazawapatsa makalatawa.

*Achinyamata a CFT ku karonga akufuna Mtambo atule pansi udindo*

achinyamata a bungwe la CFT mu boma la karonga akufuna mtsogoleri komanso Commander in Chief wa guluri a Timothy mtambo kuti atule pansi udindo  kamba koti akulowetsa gukuli Ku ndale pomwe akumapangira kampeni phungu yemwe akuimira chipani Cha MCP mubomali, a chinyamatawa ati Mtambo sakuyenera kumatero ndipo tsopano zafika potopetsa ndipo awoopseza kuti ngati satula pansi udindo iwo atuluka gukuli.

*Boma liimitsa mayeso a fomu 4*

Mayeso a Chaka chino akumana ndi mavuto ochuluka kwambiri pomwe poyamba analephereka kulembedwa mu June kamba ka mlili wa covid19 ndipo mmene tsopano anawa amafuna kuthana nazo nyasi zachitikanso pomwe mayesowa anali ponse ponse mmasamba a mchezo. Avant yapeza kuti mayesowa anatukuka kale kale ndipo ma sukulu ena mayeso awo omwe akutchedwa kuti moc anali ndi mafunso ofanana ndi omwe alembedwawa komanso Avant yapeza kuti mayesowa anatuluka bungwe la maneb lisanadindepo chidindo chawo chomaliza zomwe zikusonyeza kuti ogwira ntchito ku maneb ndi omwe anatulutsa mayesowa. Pakadali pano president Chakwera watsutsana ndi ganizo loti mayeso achibwereza alembedwe mu March koma iye wati mayesowa alembedwe mu January ndipo akulu akulu a manebu onse achotsedwe ntchito kamba koti sanathe kugwira bwino ntchito yawo.

*Anthu 11 amangidwa kamba koba zipangizo zomangira stadium ku zomba*

Apolisi ku zomba amanga anthu okwanira khumi ndi mmodzi omwe akuwaganizira kuti amaba zipangizo zomangira bwalo la mpirali ndipo apolice akwanitsa kupeza mwa zinthu Zina zomwe zinabedwazo,pakadali pano anthu ali ku ndende ya zomba komwe akusungidwa kudikira tsiku la mlandu.

*Mnyamata wa zaka zisanu wamwalira ndipo ena ali kuchipatala kamba kodya zikhawo za poizoni*

Mwana wa zaka zisanu ku dedza wamwalira komanso achibale ake ena agonekedwa mchipatala kamba kodya zikhawo zomwe akuti zinali za poizoni, anawa anadya zinthuzi kamba kanjala yomwe yavuta kwambiri pa banja lawo.

*Alimi adandaula ndi mavuto a network pogula zipangizo za ulimi zotchipa*

Anthu ochuluka mdziko muno akhala akugona mmalo ogulitsa zipangizo za ulimi zotchipa kamba kamavuto a network, ndondomekoyi ndi yamakono ndipo ikufuna kuti pasakhale chinyengo pa kagulitsidwe ka fetereza, boma lati lamva madandu a anthu ndipo  likonzamavuto onsewa pofika lamulungu pa 8 November ndipo boma la Tonse likupepetsa kwa anthu kamba ka mavutowa.
Pakadali pano anthu ena adandaula kuti ma vendor akugula ziphaso za unzika kwa anthu ndikumakagwiritsa ntchito pogula fetereza, koma boma linachenjeza kale za mchitidwe oterewu kuti akapezeka otere alandirachilango chokhwima

*Bushiri ndi nkazi wake atuluka pa belo*

Mneneri otchuka wa dziko la malawi koma amakhala ku South africa bushiri watulutsidwa pa belo pa mlandu omwe akumuzenga kamba kofuna kuzembaitsa ndalama, bwalo la mlandu kumeneko lati abushiri atulutsidwe komanso awaletsa kuchita zinthu Zina monga kulalikira moopsyeza mboni za mlanduwu, kutuluka mdziko la South Africa komanso kutuluka mdera lomwe alimo, awalanda zipaso zoyendera komanso kuti apereka chikore Cha katundu wawo komanso ndalama yokwana 200,000 rands zomwe iyewapereka.

*Magufuli apambana chisankho ku Tanzania*

Dziko la Tanzania linachititsa chisankho msabata yathayi ndipo opambana kumeneko ndi yemwe anali mtsogoleri wa dzikolo, a John pombe magufuli,Avant yapeza kuti anthu amukonda mtsogoleriyu kamba ka ulamuliro wake wabwino komanso othana ndi katangale, izitu sizinasangalatse mtsogoleri otsutsa, yemwe amafuna kuchita zionetsero ndipo anamangidwa ndi achitetezo a dzikolo kamba kozetsa chisokonezo, ku Tanzania kunalibe network ya internet kwa matsiku atatu kufikira atalengeza opambana chisankho

*Donald Trump aluza zisankho*

Avant inaliso Ku USA komwe nako kunali chisankho pomwe akulu akulu awiri omwe ndi a Donald Trump komanso a Joe Biden atengetsana koopsya kumeneko pakadali pano zaziwika tsopnao kuti  yemwe ndi president olamula mu dzikolo waluza chisankho ndipo yemwe anali wachiwiri kwa Obama  a Joe Biden ndi yemwe wapambana.   kuvota kwa mdzikolo ndi kovuta kwambiri pomwe munthu opambana akuyenera kuwina mavote okwana 270 kuchokera mmadera awo omwe alipo osachepera 500 ndipo tikunena pano Trump wapeza ma vote 214 pamene Joe Biden wapeza  mavote  284 izi zikuthandauza  kuti tsopana Joe Biden  ndi president wa USA wachinamba 46
Poyamba a trump amati chisankho sichinayende bwino ponena kuti iwo awabera koma pano awona okha okha mmene zilili ndipo avomereze kuluza kwawo.a trump akhalabe akulamulira mpaka January Chaka Cha mawa pomwe a Joe Biden azayamba ntchito yawo.

*Aphunzitsi ochonga mayeso a sitandade  8 akwiya ndi ma allowance*

Aphunzitsi omwe akuchonga mayeso a primary omwe alembedwa miyezi iwiri yapitayi akwiya ndi zomwe bungwe la manebu lachita powapatsa ndalama zochepa za ma allowance zomwe ndi 67,350 kuyerekeza ndi 77,800 yomwe amalandira Chaka chatha, aphunzitsiwa ati mmalo moti ndalama izikwera koma manebu ukuitsita ,kusawapatsa malipiro oyenera pa ntchito yawo kungathe kusokoneza kagwilidwe ka ntchito zomwe zingakhuze kakhozedwe ka anawa.

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *