Akuluakulu oyendetsa bwalo la Bingu ati mipando 70 ndi yomwe inaonongedwa ndi ochemelera ena pa mwambo otsegulira mpikisano wa Airtel Top 8 pakati pa ma timu a Silver Strikers ndi Mighty Mukuru Wanderers loweruka lapitali.
Mkulu oyang’anira bwaloli, Ambilike Mwaungulu, wauza Zodiak Lero kuti ndalama zosachepera K10 million ndi zomwe zifunikire kubwezeletsa mipandoyi kamba koti tsopano zadziwika kuti ndi mipando yambiri yomwe inaonongedwa.
Pakadali pano, bungwe la FAM lati lalandira ma lipoti onse okhudzana ndi masewerowa, amene anathera pa njira ndipo tsogolo lake lidziwika komiti yoyendetsa mipikisano ikakumana sabata ino isanathe.

Mpirawu unathera pa njira timu ya Mighty Mukuru Wanderers itakanitsitsa kuti siyipitiriza kusewera pokha-pokha referee Godfrey Nkhakananga abwezeretse chiganizo chake choyamba choyimba wenzulo kuti mpira uyime kaye.
Koma Nkhakananga anasintha chiganizochi Stein Dave atamenyera mpira mu ukonde ndipo oyimbira mpirayu anavomereza chigolichi.
