olemba DR MWALE
Avant publications yapeza kuti ntchito yomwe boma linakhazikitsa yowerenga ogwira ntchito m’boma onse ndicholinga choti athane ndi anthu omwe amangolandira ndalama koma sakugwira ntchito, ikuyenda bwino koma pomwe matsiku atsala pang’ono kuti athe ogwira ntchitowa akukakamizika kukhala ku ma office abomawa kupitiliza nthawi yogwilira ntchito
Mwachisanzo boma litalengeza kuti lichita ntchitoyi aphunzitsi,ma nurse komanso ogwira ntchito muboma onse anauzidwa kuti apititse ma certificates awo, chiphaso Cha unzika komanso chikalata chomwe anasaina poyamba ntchito (PSR19 form)
Avant inali ku Zomba komwe yaona ndi maso nkhanza zomwe ogwila ntchito mubomawa akumana nazo,
Ku zomba songani, ogwita ntchito aweruka 12 koloko usiku pomwe anali akuperekabe zimakalata zawo ku boma, malamulo a aboma amalora anthu kugwira ntchito kwa maola asanu ndi atatu,( 8 hours) ndipo aliyense akuyenera kuweruka 5koloko mazulo, koma izi sizinali chomwechi ku zomba pomwe mtolankhani wa Avant anakhala usiku onse wapa 20 October 2020 kuti awone ndondomeko yabomayi yogwilitsa ntchito anthu usikuyi pomwe zimatenga nthawi kuti amalizane ndi munthu mmodzi.
Ambiri mwa anthuwa anali azimayi omwe amadandaula za njala komanso mantha kuti ayenda bwanji popita kunyumba zawo chifukwa panthawi yomwe amamaliza (12am usiku) ma minibus anali atasiya kuyenda
Mwachidule Avant publications ikupempha boma la Tonse kuti lipepese kwa anthu omwe azunzika ndi ndondomekoyi powapatsa allowance (over time) , transport angakhalennso chipepeso chifukwa zimakhala zovuta kukafotokoza kunyumba monga munthu wa mayi kuti anali kuntchito usiku ngati uwu pomwe Tonse tikudziwa za malamulo a anthu ogwira ntchito ndi nthawi yowelukira.
Taganizani mwanyamuka 8 koloko mmawa ndipo mukubwerako 12 koloko usiku amuna kapena akazi anu aziti munalidi ku ntchito?
Pena tiyeni tizikhalako serious ngati boma ndipo tiwaganizire anthuwa ndi po khalidwe ili lisazachitikenso ndipo tiwalemekeze ogwira ntchito athu ngati nthawi yatha mawa ndi tsiku basi.
Responses
info@avantmalawi.com