Msangulutsi Emmanuella Amangira Nyumba Amayi Ake


Wolemba Wongani Chipeta

Akatswiri osiyana siyana osangalatsa anthu ayamikira mtsikana wosangalatsa anthu ndi zisudzo Emmanuella pamene wakwaniritsa kumangira amayi ake nyumba yapamwamba.

Lachisanu pa 13 November, masamba amsangulutso anali odzadza ndi zithunzi za mtsikana wazitsudzoyu pamene amaonetsa nyumba yomwe iye wamangira amayi ake. Chochititsa chidwi ndichoti mtsikanayu ali ndi zaka khumi(10).

“Ndakumangirani nyumbayi amayi chifukwa cha mapemphero anu komanso kundilimbikitsa kwanu. Ndikudziwa munkangofuna kanyumba kakang’ono, koma Emmanuella wakupangirani aka.” Anatero Emmanuella pats amba lamchezo.

Emmanuella monga mmene ambiri amamudziwira ndi zitsudzo ndi mtsikana amene dzina lake lonse ndi Emmanuella Samuel. Iye anabadwa pa 22 July, 2010 ndipo pakadali pano ali ndi zaka khumi(10).

Emmanuella amachokera ku dera la Immo( Immo State) kumwera koma chakummawa kwa dziko la Nigeria.

Kuchokera mchaka cha 2016, Emmanuella wapatapo mphoto zosiyana siyana. Iye wapatsidwapo mphoto yokhala katswiri woposa anzake onse oyamba kumene zitsudzo zoseketsa. Kenaka walandiraponso mphoto yokhala Mfumukazi ya zitsudzo zoseketsa ya Afro-Australian Music and Movie Awards ndi bungwe la ku Australia.

Tsamba lapa internet la You Tube linaperekanso ulemu kwa Emmanuella pokhala ndi otsatira ochuluka. Mu 2016 mokha zitsudzo za Emmanuella zinali ndi anthu opos a 6 million.

Emmanuella anatchuka kwambiri ndi sewero lomwe pachingerezi amati, “This Is Not My Face Oh” kutanthauza kuti “Iyi Sinkhope Yanga” pamene amakamba za mphunzitisi wamkazi woyang’anira sukulu yawo.

Mtsikanayu wapambanaponso mphoto zina zikulu zikulu kupatula zimene zatchulidwazi.

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *