HEALTH TIP

KUMVA KUWAWA POKODZA

Olemba DR MWALE

Mavuto a kumva kuwawa pokodza akumachulukira makamaka kwa azibambo matsiku ano. Ndipo munthu akayamba kumva zizindikilo zomamva kuwawa amakhala kuti akudabwa kuti Kodi zimenezi ndi zichani? Ndipo vuto ndi chani.
Ndikunena pano alipo ena omwe ali ndi vuto Ili koma sakudziwa kuti angathane nalo bwanji.

KODI CHIMAYAMBITSA KUWAWAKU NDI CHANI?

Mavuto akumva kuwawa pokodza akakhala mwana timati ndi likodzo ndipo akulu akulu nawo amaganizanso choncho koma mwana ndi munthu wankulu ndi zosiyanasiyana , wankulu akamamva kuwawa ndekuti masozi (muscles) yomwe imatseka pa khomo la chikhodzodzo yayamba kufinya mopyola muyezo. Masozi imeneyi imatchedwa kuti sphincter muscles ndipo kuti iyambekufinya kwambiri ndekuti ma glands omwe akuwapanga support akunenepa kwambiri omwe timawatcha kuti ma prostrate glands,
Ma glands amenewa akamakula chifukwa Cha zimafuta zomwe timadya komanso kukula mu zaka zathu amatha kufinya njira yodutsa mikodzo apa ndi pomwe anthu ena amamva kupweteka,

Ukadziwe bwanji kuti ma glands ako akukula?

Utha kudziwa kuti ma glands akukula mnjira zotere

1: umatenga nthawi kuti mikodzo ituluke, ndipo umamva kuwawa.

2: mikodzo ikumatuluka yotentha kwambiri ndipo zimapweteka.

3: mikodzo simagwa patali. Kusonyeza kuti ikutula yopanda mphamvu.

4: imatha kutuluka iwe utamaliza kale kukodza ndipo umatha kuzikodzera mkabula.

5: sumakhala ndi chilako lako Cha ku bedi ndipo chikakupeza umafookera mnjira umuna osatuluka

Mavutowa amakonda kuchitika kwa anthu omwe zaka zawo zadutsa 40 koma matsiku ano kamba ka dzakudya zosiyanasiyana anthu ena a zaka 30 amatha kudwala matendawa.

Nthawi Zina chifukwa cholephera www.avantmalawi.com kukodza bwinobwino mikodzo imakaundana mu chikhodzodzo zomwe zimapangitsa kuti muzipanga timibulu mkati mwa chikhodzodzo zomwe kuchipatala amati ndi ma bladder stones( mwala mu chikhodzodzo)

dziwani izi

Mavutowa mukawalekerera ndi pomwe mumaona kuti kuchipatala akuikani chubu choti muzikozeramo kwinaku atakupangani operation. Ndikhulupira kuti munaonapo izi.

Akakhala azimayi iwo amangomva kutentha potaya madzi , amakhala ngati akukodza madzi a moto, zomwe zimatsautsa ndipo amakhala ngati awathira mchere malo obisika, ngati sasamba changu samva bwino. Mukaona izi zikuchika azimayi samalani ndipo pezani thandizo mwachangu.

Mavuto amenewa nthawi Zina amabwera kwa achinyamata(akazi ndi amuna) kamba kogonana mosaziteteza, zogwilitsa ntchito monga ma tissue komanso ma pads ena amakhala kuti muli chemical yomwe sikugwilizana ndi thupi lanu.

Muli ndi vuto lakumva ululu pokodza ndipo mwayesa zavuta?

Contact 0991259788/0881893355

www.avantmalawi.com

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *