Timu ya Flames inanyamuka kupita ku Cameroon komwe ikachite nawo masewera a mu chikho cha matimu amu africa. Timuyi inanyamuka ndi mphunzitsi wachizungu a Mario Mariana Marinica (MMM)
Zaziwika tsopano kuti muli kusagwirizana mu camp ya flames pomwe osewera ena sakukondwa naye mphunzitsi wa timu yadziko linoyu.
Osewerawa ati mphunzitsiyu akumagwilisa ntchito mau osakhala bwino (kutukwana – use of vulgar words) kwa osewera komaso sitayilo yake yomwe akufuna kuti anyamatawa azigwiritsa ntchito posewera siyabwino ndipo anyamata ena sakufuna ponena kuti ziwatengera nthawi kuti azolowere pomwe mpikisanawu wayandikira kale.
Meke Mwase ndi mphunzitsi yemwe anapangitsa kuti timuyi ipite ku mpikisanawu koma zinadabwitsa anthu pomva zoti FAM yamuchotsa ndipo yapereka ntchitoyi kwa mzunguyu.
www.avantmalawi.com
VINJERU NGWIRA