Loto la mtsogoleri wa kale wa dziko lino malemu Bingu Wa Mutharika loti Malawi akhale ndi bwalo lochitirapo masewero osiyanasiyana ngakhale linapherezeka koma zikuonetsa kuti pano bwaloli lasanduka bwinja kamba kosowa chisamaliro.
Malemu Bingu ankafuna bwaloli limangidwe mu nzinda wa Blantyre ndicholinga choti lizikhala likugwiritsidwa ntchito pafupipafupi ndi timu ya dziko lino ya Flames komanso ma team monga Nyasa Big Bullets ndi Mighty Wanderers omwe mpakana lero alibe ma bwalo awo.
Koma kutsatira imfa ya Bingu, boma la Joyce Banda lidasintha ganizo lomanga bwaloli ku Blantyre ndikukamanga ku Lilongwe komwe ma timu akumeneko ali kale ndi ma bwalo awo awo zomwe zikuchititsa kuti bwalo la Bingu lizingokhala popanda zochitika komanso angakhale timu ya Flames imasewera ku bwalo la Kamuzu ku Blantyre nthawi zambiri.
Anthu wokonda masewero mu dziko muno ati ndiwokhumudwa ndimene boma likuchitira pano posasamala bwaloli lomwe ndila mtengo wapatali komanso lalikulu mu dziko muno.
Ambiri mwa iwo akuti bwaloli inamangidwa kolakwika potengera kuti likanakhala mu nzinda wa Blantyre sibwenzi kukusowa masewero chonchi chifukwa ma timu aku Blantyre bwenzi akuyigwiritsa ntchito kwambiri.
Bwalo la Bingu limanyamula anthu oposa 40,000 koma kamba kongokhala masiku apitawa boma linasandutsa chipatala chosungirako anthu odwala mlili wa Covid – 19.
Dreaming in colors. The dreamer is dead