Posachedwapa takupasirani nkhani yoti yoti mzondi mkandawire wamangidwa ku karonga.
Malingana ndi malipoti akuonetsa kuti ku karonga komwe kukufuna kuchitika chisankho chapadera kunali zipolowe dzulo.
Koma malingana ndi kafukufuku zipolowe zinakhuza zipani zonse ziwiri zolamula.
Avant Publications inali konko ndipo inachita machawi kufunsa mbali zonse ziwiri za mpungwepungwewewu.
Malingana ndi achinyamata a UTM akuti anamvetsedwa kuti gulu la MCP lasonkhana pa sukulu iina usiku ndicholinga cholita kapeni usiku wakhomo ndi khomo ndicholinga choti agawe ndalama, zomwe zili zosaloledwa komanso poti kampeni añatseka kale, apa ndipomwe gulu la UTM motsogzedwa ndi mzondi mkandawire komanso mnyamata yemwe akuziwika kuti FIDOMAN anapita kukawafunsa chimene amachita anthuwo usiku pamalopo, ndipo a MCP pokwiya ndikubwera kwa anthuwa anagwira fidoman ndikuyamba kumumenya mpaka anakuwa kufuna chithandizo kwa anthu.
Avant publications sinalekere pompa koma kumvanso mbali ya achinyamata a MCP omwe iwo ati iwo akuganiza kuti achinyamata a UTM anali ndi kaduka chabe chifukwa Cha kampeni ya mphamvu yomwe nduna yoona zachitetezo mdziko muno a chimwendo Banda anachita mderalo ndipo Iwo akuti a UTM amafuna achitire chiwembu ndunayi zomwe zinawakwiyitsa ndipo iwo anakwiya.
Apa panali ndewu ndikuyamba kuphwanya zithu komanso kupweteka anthu komanso atsosogoleri achipani monga a hon Paul khoma,Hon Gerald kapiseni komanso hon Jephtar Mwale.
Koma achinyamata a UTM i wo anenetsa kuti cholinga Chawo chinali kukaonetsetsa kuti palibe akuchita kampeni usiku ngati monga momwe zinakhalapira chisankho chapadera chapitachi kukaronga komweko.
Malingana ndi malipoti ena zikuoneka kuti mzondi mkandawire wamangidwa kamba koti amajambula zithuzi nthawi yomwe izi zimachitika. Zomwe anthu ena akuganiza kuti akufuna kubisa umboni.
Sitingakambe za kuwina kwa MCP kukhala olamula lero opanda UTM ndipo UTM singakambe zachipambano chake kumpoto kopanda kutchula dzina la mzondi mkandawire. Ndipo Tonse alliance payokha ikudziwa bwino za mzondi mkandawire
Mpando wa phungu mmodzi asangawanitse Tonse alliance ndipo UTM ndi MCP onse akuyenera kudziwa kuti kopanda wina, winayo sakanawina payekha.
www.avantmalawi.com
*DR MWALE*