KUSAKA CHIPULUMUTSO KWAPONYEREDWA KWAKUYA KU MALAWI

“Ngati tinena kuti ndife olungama tizinamiza tokha, pakuti Tonse tinachimwa naperewera pamaso pa mulungu.”

Awa ndimawu omwe timawapeza m’buku lopatulika, ndipo pofuna kukwaniritsa malemba azitumiki akuyesetsa kuchita zithu zoti tikalowe mu ufumu wakumwamba.

M’busa  wa mpingo wa Living fountain church anapachika nyama yaiwisi mkachisi mwake ndikuyamba kudya nyamayo komanso kumwa magazi ake. Iye anaoneka akudya nyama komanso kumwa magazi ndipo anauza akhilisitu ake kuti nawo atero ndipo ambiri mwa Iwo anagwada ndikumwa magaziwo.(azimayi a mvano)

Abusawa achita izi ponena kuti kumwa magazi komanso kudya nyama yayiwisi yopachikidwa pantanda kukuthandauza mwazi komanso thupi la ambuye yesu pa ntanda.

Aka ndikoyamba kuti izi zichitike mu tchalitchi ndipo zayambira kuno kumalawi. Mpingo yambiri ikukumbukira mwambo onga uwu pomwa vinyo komanso kudya nkate zomwe zikuthandauza kukumbukira thupi la ambuye yesu.

Zonse zimayamba ndi Inu. Ndipo chikhulupiriro chanu chikakupulumutsani

www.avantmalawi.com

*DR MWALE*

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *