*loweruka lililonse pano pa avant publication tidzimva nkhani zosiyanasiyana zochokera madera apadziko lapansi*
Tiyambe ndi kwathu kuno ndipo tilowere kubangula mkulu wina waona mazangazime ng’ona itamuonetsa zakuda, mkuluyi yemwe wakhala akupha nsomba mu tsinje wa Shire anapeza ng’ona itang’amba khoka yake ndikumadya nsomba zomwe zinali mukhokamo, mkuluyi bambo Simoni Mkwembelera ataona izi anadzadzidwa ndi mkwiyo ndipo anagwera pomwe panali ng’onayi mkuyamba kumenyana nayo, ng’onayi ikathawira mbali ina mkuluyi amaitsatira kwinaku akulalatira ng’onayo, Komabe bambo Mkwembelera adachepera mphamvu mpaka anavulazidwa dzanja, mwendo ndi kumsana, panopa mkuluyi akulandira thandizo lamankhwala kuchipatala chapaboma kunsanje anthu achifundo atamupulumutsa kuchilombocho.
Kunsanjeko komweko mdera la TA Mlolo kufatima mmudzi mwa Mlambala nkhalamba ina yomwe imangotchedwa kuti mayi Zitatu yakhala ikulankhula modzitama kuti mvula siigwa kudelari ngati anthu sapanga zomwe iyo inganene. Mayi Zitatu anadabwitsa anthu atanena kuti masiku ake omwalira atsala ochepa ndipo mvula igwa iyeyo akamwalira, ndipo ngati anthu akuyenera kukamumangira mnyumba kufupi ndi mtsinje wa Shire poti akuti akadzamwalira adzasunduka Napolo ndipo kuti zinthu zisaonongeke iyeyo akuyenera kumangilidwa nyumba kufupi ndi mtsinje osati kukhala kumtunda. Mvula yakhala ikuvutadi kwanthawi yayitali pofikira pa 22 December pomwe anthu olusa anakayatsa moto mnyumba ya Mayi Zitatu iwo alimomwemo koma zodabwitsa zidapezeka nkhalambayi idapezeka ili panja poteropo komanso ili moyo. Izi zidapangitsa mamulumuzana kugundana mitu ndipo adagwirizana kupanga zomwe nkhalambayi idanena, ndipo mafumu adalamula azimayi ndi azibambo kukamanga nyumba kudambo kenako GVH Msambo adabwera kudzanyamula nkhalambayi panjinga yake molamulidwa ndi TA Mlolo kukamusiya kunyumba yanyowaniyo usiku watsikuli mvula idachezera padenga, nkhalambayi yakhalanso ikunena kuti madzi osefukira amchaka cha 2015 adali ng’ono wake wankhalambayi.
Ku Rumphi Mzibambo wina moyo wake uli mwakayakaya atayambana ndi mfumu ina kumeneko.
Nkhani yonse ikuti bambo Felix Nyirenda adapalamula mlandu wosapita kuchitukuko ndipo mfumu yamudzimo idakokera bamboyu kubwalo lake, koma nkhani ili mkati bambo nyirenda adapsa mtima ndi kunyoza kochokera pakamwa pa mfumu Hifwana ndipo idapita pafupi ndi mfumuyi mkuivula chipewa chake chomwe idavala kenaka bambo Nyirenda adavala chipewacho, atangovala adayamba kumva mutu ndipo adavula chipewacho koma panthawiyi zodabwitsa zidaoneka mmutu mwa bambo Nyirenda poti mudameteka mpala ndipo mudali nthunzi yamagazi ponseponse. Anthu ambiri adandaula chifukwa chazamatsenga zomwe mfumuyi yakhala ikupanga poti akuti simatha kuzenga milandu koma imadalira ufiti!!!!.
Tiyeni tilowe mmayiko akunja timveko ziwiri zitatu.
Ku Cape town mdziko la South Africa mu town ya Lesssaburg banja lina latekeseka kumeneko kamba ka zomwe wachita mamuna wa m’banjamo. A Zuwyenda akuti adakatenga ngongole Ku banki ina kumeneko mogwirizana ndi akazi awo kuti ayambire bizinesi, koma ma mkuluyi ali mtawoni adamva zoti mabokosi amaliro atsala ochepa mderali ndipoa Zuwyenda adangoganiza zogula mabokosi okwanira banja lawo kuti akasunge kuti akamwalira asadzapite ngati nkhumba. Bambo Zuwyenda adakwezetsa mabokosiwa ulendo kunyumba atawafundira ndi lona ndipo mkazi atamva hutala adatuluka panja ndi chimwemwe ndipo ataona galimoto lodzadzali akuti chimwemwe chidali mtsaya kuti amuna awo awoda bizinesi, koma akuti nkhope ya Jaquelin idasintha pomwe eni agalimotowa amamasula lona kuona mabokosi okwana 7 ndipo mkazi atafunsa mamuna wawo adayankha mmaso muli gwaa!! kuti matenda a Corona sasiya wina aliyense ndee ndi bwino kukonzekeratu!!! Panopa Jaquelin wanyamula katundu wake yense komanso ana onse kuwasiya Mr Zuywenda ndi mabokosi awowa!!!!
Nako Ku China mzimayi wina wadya mwa wake kuyesa nyama yankhumba. Mayi Hengch Chunahg womwe ndi akhungu kapena kuti wosaona akuti akhala akukonda kumadya tiwana tankhumba moyo wawo kwanthawi yayitali. Mayiwa womwe amuna awo adawathawa kamba kotchuka ndi zamatsenga ati adapeza mwana wawo atagona pafupi ndi pomwe akhala akudyetsera nkhumba zawo, Iwo adangogwira mwanayo mkukamuponya mu frying pan yayikulu monga momwe akhala akuchitira nthawi zonse ndipo akatero akuti amachotsa chiwalo chimodzichimodzi mkumakhwasula koma panthawi adazizwa kuti adya mwana wawo pomwe adagwira mutu wamwanayi miyendo ndi manja atamaliza kale, wantchito wawo panthawiyi akuti adali kumalo ayekha poti akuti adapezeka ndi nthenda ya Covid 19.
Ndipo mudziko la South Sudan kudera lina chakumpoto kwadzikoli akuti kwabuka matenda ena achilendo kumeneko ndipo akusowetsa anthu mtendere, malingana ndi mtolankhani wa Sudanese Fact Publications wati nthendayi yomwe ikungotchedwa syuilipi kutanthauza kuti kalikokha ikugwira kwambiri anthu omwe sali pabanja ndipo mankhwala ake mkungogonana ndi munthu ikumachepa mphamvu!!! Sudanese fact publications yati yawona azimayi ambiri akuchengetera amuna awo nawonso amuna akupereka chikondi chokwanira kwa akazi awo kuti atetezeke kunthendayi, panopa pafupi azimayi okwana 3756 mderali akuti atenga pakati kwa mwezi umodzi wokha!!! Panopa boma lagawa makondomu ochuruka kuderali.
Mdziko la India Mizukwa ina yalengeza za ukwati wawo womwe ukachitikire chakumadzulo kwamzinda wina waukulu dzikomo. Anthu akuti akhala akukumana ndizodabwitsa maka oyenda usiku pomwe akhala akuimitsidwa ndi zinthu zosaoneka bwino pomwe ndipo zakhala zikugawa makalata aukwati wawo womwe udzachitike pa lamulungu pa 7 February. Mizukwayi yakhala ikugawa makalata kwa atolankhani kuwapempha kuti akalengezetse zaukwatiwo pawayilesi zawo za ukwati wa Linisy ndi Hettah.
Timalize ulendo wathu walero ndi mdziko la Thailand pomwe Mphunzitsi walamulidwa kuti aphedwe mwankhanza kapena kukagwira ukayidi kwa zaka 234 chifukwa chogonana ndi kupereka mimba kwa atsikana onse amkalasi mwake!!! Magistrate yemwe amaweruza nkhaniyi wati Pedwz wakhala akugwililira ophunzira okwana 78 achitsikana kuyambira chaka chatha omwe amayimba form 4 pa sukulu pomwe amaphunzitsa mkuluyi ndipo ophunzira okwana khumi ndi atatu (13) ali ndi ana ndipo otsalawo 65 ali ndi mimba za mkuluyi. Ophunzirawa adandaula chifuwa chakumangidwa kwamkuluyi.
Apanso ndee pamapeto athu mutsiku lalero, mukhale ndi tsiku lopambana!!!
*Angozo kafu_K Peter*
Avant publication shares
@ avantmalawi.com