CHAKA CHOPAMBANA CHATSOPANO-2021

AVANT PUBLICATIONS

BYE BYE 2020

Unali ulendo wautali kuchokera mu 2019 pomwe group ili linadziwika kwambiri ndicholinga chodziwitsana mmene zinthu zikuyendera mdziko mwanthu komanso mmene mlandu wa chisankho umayendera. Zinatengera chisomo cha mulungu kuti tonse tinadutsa zaka zimenezi ndipo lero ndi ife tikumaliza nawo chakachi mulungu alemekezeke.

Tithokoze nonse amene mwakhala nafe kuyambira pa chiyambi kufika lero. Ena anatijoina nkuchoka koma inu mulipobe mulungu alemekezeke.

Group lino limatumiza nkhani zomwe zili zoona komanso zolembedwa bwino ndi atolankhani omwe ali ndi luso lothyakuka ndipo ngati mwamva nkhani koma mukuikaikira yambani mwadekha ndikudikira Avant publications kuti itsindikize Kaye musanayambe kutumizira anzanu chifukwa ife tili pano kutsindikiza nkhani zoona zokha zokha.

Pakadali pano Avant Publications ndi nyumba yomwe ikufalitsa nkhani mwachangu ndipo tikupezeka mmaboma onse a mdziko muno komanso maiko akunja. Muthakutipeza pa whatsapp,Facebook komanso pa website yathu yomwe ndi www.avantmalawi.com

Tithokoze nonse amene mwakhala mukuthandiza ndi information yosiyanasiyana komanso angakhale kutumiza ndalama ya bundle mulungu akudalitseni.

Kwa onse owerenga ,oyika ndemanga komanso otumiza nkhani zosiyanasiyana tikuti musasiye pitilizani mulungu akudalitseni.

Pomaliza ma admin onse aku avant akufunira membala wina aliyense mu group muno mafuno abwino achaka Cha tsopano, ambuye akudalireni.

2021 tibweretsako tima audio tingapo ta momwe mulandu wachisankho unayendera ku khoti
Koma padzakhala kufotokozera 🤣🤣🤣

Bye bye 2020 and welcome 2021

DR MWALE

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *