AWOTCHEDWA KAMBA KOBA NG’OMBE

Munthu wina yemwe wakhala akuba ng’ombe mmakola a eni ku monkey Bay kumangocchi wagwidwa lero.

Chomwe chinachitika ndi choti mkulu wina yemwe dzina lake ndi Jasten wa mmudzi mwa kamangazula kumangochi anali ndi mchitudwe oba ng’ombe za wanthu ndikumakagulitsa. Iyeyu amatha kubwera ndikuzapanga ngati wogula kuzafunsa mtengo kenako kumapita komma kuli kuzayendera kuti mazulo azabe bwino. Mkuluyi wakhala akuchita izi kwa nthawi yaitali ndipo anthu amamuopa , zomwe zinapangitsa kuti azichita zinthuzi mosabitsa koma kumaba mosanyengerera.

Awotchedwa kamba koba ng’ombe

Usiku wathawu anakaba mmudzi wina wa a matola ndipo anthu kumeneko anamemana ndikumugwila. Atazindikila kuti ndi iyeyo sanachitilenso mwina koma kusonkhanitsa mateyala ndikumuyatsa kamba koti atopa nayo.

A Justin anakwatila pamudzi wa a Nikidzi muderalo.

Anthu ambili akumafika potengera malamulo mmanja kamba koti opalamulawo amakhala kuti akagwidwa sachedwa kutuluka kundende.

Kanemayu wamantha asaonere ku comment section

Avant publications

DR MWALE

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *