MAFUMU, AMIPINGO OSALOWERERA NDALE

Akatswiri pa ndale mdziko muno apempha azitsogoleri a Mipingo komanso mafumu kuti akhale osamala mmachitidwe komanso malankhuludwe awo pa nkhani za ndale.

Mawuwa adza kamba ka zomwe azibusa komanso mafumu ena akhala akulankhula pomwe amakunana ndi a president a dziko lino kunyumba yachifumu mu mzinda wa Blantyre.

Apostle Samuel Vikhumbo anatsogolera azibusa ena kukakumana ndi mtsogoleriyu kumene anakalimbikitsa Pulezidenti wa dziko a Dr Lazarus Chakwera kuzayimanso mu 2025. “Bwana anthu akukondwera ndi ntchito zanu za chitukuko choncho musasole kuti utsogoleri wanu muusiyiĺe panjira”

pakuzukuta malankhulidwewa, a Katswiri ena pa ndale ati ngakhale kuli kwabwino a mipingo kukhala mbali yopembedzera utsogoleri wadziko lino koma a Mipingo azikhala ndi malire poyikapo mlomo pa nkhani za ndale. Iwo ati “mawu oterewa akuonetseratu kuti akufuna achakwera azaimilenso mgwilizano wa Tonse mu 2025 kuiwala zoti zipanizi zili pa mgwilizano. Kuuza achakwera kuti asalore kuti chitukuko achisiyile panjira kuli ngati kulowerera ndewu ya eni zomwe sizabwino kuchokera kwa mafumu ndi amipingo. Zikanakhala kuti MCP silipa mgwlilizano zinali zomveka koma poti mafumu ndi amipingo onse akudziwa kuti MCP ili pa mgwilizano kulankhula kotereku nkozetsa udani mmalo momanga. Gwilani ntchito ndi boma lolamula koma musalowere ndale” aterewo akatswiliwa.

Avant publications

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *