President wadziko lino pa 15 november alankhula motere ku mtundu wa amalawi
A president akuti iwo akudziwa kuti a malawi akudutsa mu nyengo zowawa maka kamba ka kugwa kwa kwacha. Choncho pachifukwa ichi iwo ati ayika njira izi kuti amalawi asamve kuwawa
Choyamba iwo ayimika ma ulendo awo onse akunja mpaka mu March. Izi zikuyamba ndi ulendo wapa 28 pano. Omwr amafuna kupita kunja.
● Onse omwe amafuna kupita kunja pa misonkho ya amalawi asayendenso ndipo onse omwe ali kunja abwereko msanga akamva uthengawu.
●Onse omwe amalandila ndalamazogua mafuta kuchokera kuboma onsewo azilandila half ya mafutawo.
●Onse ochita maseminary a boma awonetsese kuti seminary imeneyo ikhale yaphindunkomahso aziziwitsa kaye a president ndiponma allowance sazipereka chisawawa ndizopanda pake zomwe
●Nduna ya zachuma iyike ndalama zowonjezera kwa ogwira ntchito muboma komanso ayikemo ndalama za ngongole kwa anthu ochita business. izi siziyambika oano koma mu budget ikubwerayo ndipo zizayamba budget ikadutsa. Koma sananene kuti azaonjezera ndi ma percent angati.
●Nduna ya zachuma iwonetsetse kuti ikuyendera ma business kuti awoneserse kuti ogulitsa sakukwera mtengo moonjezera. Ndipo azipereka report kwa president sabata iliyonse
●A water board asakweze madzi ndipo ndalama zomwe zilipo za Waterboard agwiritse ntchito zomwezo pa poyendetsera bungweli koma madzi asakwezedwe kamba koti madzi ndi moyo.
●Ndalama zonse zomwe zapulumutsidwa ku maulendo a Apresident zigwilitsidwe ntchito pogula fetereza. Ndi kumupereka kwa amalawi kuti onse agule fetereza ndikulimira nyengo ino ya mvula
●Enanu musachite dala zosokoneza zomwe boma lakonza chifukwa lamulo ligwira ntchito pa inu.
Zikomo.
www.avantmalawi.com
DR MWALE