KATALATA KWA A PRESIDENT MUSANATILANKHULE LERO

Okondedwa president athu. Pamodzi ndi nduna zanu m’mene mukuyendetsera boma.

Ndafuna kukuyankhulani musanatiyankhule mazulo ano kuti mwina mu mfundo zanga zopanda nzeruzi zingathe kusangalasapo amalawi ndikuwaombola pa zinthu Zina.

Ndalama ya kwacha yagwa ndipo chifukwa chake mwati mukuipatsa mphavu yeniyeni yomwe imafunika kuti ikhale nayo. Ife tadandaula pa nkhaniyi koma opanga chiganizo ndinu ndipo palibenso kubweza zachitika zachitika basi.

Ife tamva zomwe boma lanena komanso laika pofuna kuti amalawi tisafinyike ndi devaluation. Mwati mtukula pakhomo kwa anthu 184 920 omwe azilandila 50,000 kwa miyezi itatu , awatu ndi anthu okha okha omwe anakhuzidwa ndi namondwe, nde funso nkumati kodi devaluation ikukhudza anthu okhawa? Ndipo devaluation kwa iwo ichitika miyezi itatu yokha? Boma lanu latinso mabanja 105,000 okhala mmatawuni azilandila 150,000 pamwezi, sitikudziwa kuti kwa miyezi ingati. Kodi devaluation izichitika kwa anthu okhawa mtawunimooo? Nanga munthu waku Dunduzu, kafukule, waku mzenga ku nkhataby, wakwa bvubwe, nanga ku walilanji , nanga wakwa msudwe kapena ku mphepo zinayi ku ntcheu azitani? Iwowa si amalawi kapena?

Apatu a president chiganizo ichi boma lanu silinapange bwino chifukwa mwapereka tsankho. Tangoganizani mabanja olandila ndalamawo muziwalemba bwanji? Sipazikhala chinyengo komanso ma udani? Chabwino inuyo mutapeza ma voti kwa anthu omwe boma lanu liziwa patsa ndalamazi muzawina? Simukuona kuti mukuzionongera tsogolo lanu?

Inetu maganizo anga ndi awa omwe ndafuna kuti mukanawaganizira ndikuwachita musanatilankhule mazulo ano

Poyamba onani zinthu zofunikira kwambiri pa moyo wa munthu . Mafuta a galimoto, sugar, sopo, mafuta ozolola, fetereza, magetsi, mchere, ndi madzi. Zinthu zimenezi sitingazithawe pa moyo wa tsiku ndi tsiku.

Boma lanu likuyenera litenge ndalama ya misonkho yathu amalawi lipereke ku ma kampani omwe akupanga izi kuti kwa zaka ziwiwi iwo atsitse mitengo ya zinthu zimenezi ndi half down. Kaya zidula ndalama zichuluka koma zipindulira tonse ndipo misonkho yathu ikhala kuti yagwira ntchito moyenera kusiyana ndikuti izingogwilitsidwa ntchito poyenda ndikubedwa ndi anthu ochepa. Kwezani malipiro a anthu ogwira ntchito muboma komanso lamulani ma kampani akweze malipiro a anthu awo molingana ndi devaluation %.

Kambilani nawo ma kampani pa za izi mumve akufuna chani ndipo angatani kuti izi zitheke. Kuli bwino kubwereka ndalama ku ma bank kupangira zimenezi chifukwa aliyense awona phindu la ndalamazo

Inuyo kungotero anthu azaiwalako za mavuto enawa ndipo Bata libwerera.

Bwana president komanso nduna zanu zonse, ndakusokoserani nkulira mutamva gwilitsani ntchito nzeru komanso misonkho yathu bwino.

Zikomo.

DR MWALE

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *