Nellie kumwenda ndi mtsikana yemwe anabadwa bwino bwino mu banja la a kumwenda mchigawo cha kumpoto ku mzimba. Iyeyu anabadawa okongola kwambiri ndipo anali ndi khumbo khumbo lofuna kupita patsogolo ndi maphunzilo ake atangobadwa. Koma khumbo khumbo lakeli linadulidwa nsonga kamba ka chithu China chomwe chinamuchitikira mu chaka cha 2011.
Linali tsiku lachiwili Pa 2 June 2011 kunacha bwino bwino ku bwengu komwe iye amakhala. monga masiku onse Nellie anadzuka monga kale nkuyamba kugwila ntchito zapakhomo. Itafika nthawi yophika Nellie anasonkha moto wa nkhuni kuti aphike chakudya. Ali mkati motakata Iyeyu anaona munthu wina akumugwira mkono wa manzere nkumuika pa moto. Apa iye amaona kuti akupsya koma samamva kuwawa kulikonse ndipo iye amaona ngati akulota. Patapita kanthawi munthu uja anazamutseka maso ndipo iye anayamba kuona mdima, pamenepa anamukoka mutu ndikumuika pamoto paja. Nellie anayamba kupsya nkhope, nkhosi komanso mthupi mose.
Nellie amaona kuti akupsya koma analibe mphamvu yoti achoke pamotopo komanso chodabwitsa choti iye samamva kuwawa. Kenako mwadzidzidzi munthu uja anamuchokera ndikumusiya pompo.
Pomwe zimachitika izi nkuti Nellie aliko yekha kunyumbako.Anthu ena omwe amadutsa munsewu ndiwo anamva fungo la chinthu chopyerera lomwe limamveka kwambiri ndipo iwo anakhota kuti akaone chomwe chimapsyacho ,apa ndi pomwe anaona Nellie ali lamba pa moto uku akupsya modetsa nkhawa. Anthuwo anamutchotsa msanga ndikumufunsa kuti chachitika ndi chani? Iye amamva koma analibe mphamvu yoti angayankhile kotero amangowayang’ana anthu aja.
Mwamachawi anamutengera kuchipata chachikulu cha muboma la Rumphi komwe madotolo atamuona anamutumiza ku mzuzu central hospital ponena kuti munthuyi wampsya kwambiri.
Ku mzuzu anamuthandiza ndipo anakhala nthawi yaitali mchipatala kufikila atachila. Kamba ka luntha komanso ukadaulo wa madotolo akuchipatala cha mzuzu anayesesa kupereka thandizo lonse lomwe limafunika kuti Nellie apeze bwino ndipo zinathekadi koma munthuyu anatsala ndi chipsyera chachikulu kwambiri kunkhope yake yonse, khosi mthupi komanso kulumala dzanja. Madotolowa atamuona ndi mmene akuonekera Nellie anamuuza kuti iye kuti azakhale bwino akuyenera kupita kunja kuti akamupange plastic surgery kapena kuti akachotse nkhungu lake lakupsyalo akaikepo nkhungu Lina. Koma kuti izi zichitike pakufunika ndalama zochuluka kwambiri zopesera 500, million.
Nkhaniyi inawakulira makolo akewo poti analibe mtengo wogwira. Anthuwa anayesesa kwa anthu akufuna kwabwino kuti awathandize koma sizinaphule kanthu.
Mfumu ya ndondo ya kwawo a TA Jalavikuwa inaitanitsa wailesi ya kanena ya MBC kuti ijambule mtsikanayu kuti mwina angapeze thandizo koma sipadapezeke angakhale khobidi. Mtsikanayu Sanagonje kuyang’ana thandizo ndipo anapitanso ku mibawa tv komwe atamujambula anthu akufuna kwambwino anamuthandiza ndi ndalama yokwana 150, kwacha yokha basi. Nellie akuyamika makanema awiriwa kamba ka luntha lawo lofuna kumuthandiza koma zavuta ndipo.
Lelo Nellie anafika ku Avant publications komwe anakumana ndi mtola.nkhani wanthu Vinjeru Ngwira ndikumuyalira nkhani yonseyi kuti mwina ngati alipo akufuna kwabwino amuthandize magawo angapo.
Choyamba Nellie anafotokoza kuti iye amakhala moyo ovutika kwambiri kamba koti pano akungokhala ndi mayi ake omwenso ndi Osauka kwambiri ndipo sakumatha kupeza olo chakudya choti adye pakhomo. “Ndikulankhula pano ndi inu ine sindinadye kalikonse kuchokera mmawa” anatero Nellie.
Moyo wanga ndikumankhala odzuzinka kamba koti anzanga ambiri omwe ndimacheza nawo amandiseka ponena kuti ndikuwaopsya, sangacheze nane komanso ndikuwabowa. Izi zikupangitsa kuti ndizikhala ndekha opanda ocheza naye. Kunena zoona zikumandipatsa maganizo moti ndimalakalaka kuti nditangofa ndiyiwale chitonzochi. Pena ndimaona ngati Bola ndingozipha kuti anthuwa ndisamawanyase.
Mtima ofuna kupita ku school ndili nawo ndipo ndikulakalaka nditatero koma ondilipilira school fees ndilibe. Inde anthu amandisala olo ku school atha kumakandisalanso chifukwa zinachitikapo kale koma ine olo ku school ya anthu omwe ali ndi zilema ija ine nditha kupita cholinga ndikapeze maphunziro oyenera kuti mwina kachakudya kokha pakhomo ndizitha kumazakapeza mtsogolomu chifukwa ndikudziwa kuti mulungu ali nane cholinga.
Kotero ngati Boma kapena anthu akufuna kwabwino angandithandize pa maphunzilopa nditha kukhala osangala.
“Ndili pano sindikupanga chilichonse nde thandizo ndilovuta kupeza sindinganene kuti anthu azindithandiza tsiku lililonse ndi ndalama ayi koma ndikufuna ndikhale ndi luso loti nane ndizikwanilitsa kupezera chakudya pakhomo panga, ndipempho langa ku boma komanso mtundu wa amalawi ndigwileni dzanja pondipititsa ku school kapena kundipatsa thandizo loti lizandithandie pa mawa.” Anatero Nellii kumwenda akugwetsa misonzi
Avant publications itamva nkhaniyi inachita chidwi kwambiri ndipo yachiona chanzeru kuti kuti tigawane ndi amalawi ochuluka omwe angathe kumugwira dzanja mtsikanayu. Boma la malawi kudzera ku nthambi ya DODMA, iyang’aneni nkhaniyi ngati ngozi yogwa mwadzidzidzi, mabungwe azachifundo tiyeni tigwirane manja pa nkhaniyi. Abungwe la TEVETA mtsikanayu akufuna luso lapadera atha kukwanitsa muyang’aneni. Boma la malawi kuzera ku ma program a anthu a disabilities mpititseni ku masukulu amenewo mtsikanayu kuti naye loto lake likwanilitsidwe. Amipingo kudzera ku ntchito za chifundo Nellie akusowekera maphunziro ,zakudya ndi malangizo kuti chitonzo chake chichoke.
Anzathu nonse omwe mulungu anakudalitsani kopambana tambatsulani zanja lanu pa mtsikanayu. Mmalawi aliyense yemwe wamva nkhaniyi ali ndikuthekera komugwira dzana Nellie. Kochepa komwe muli nako Nellie komanso Avant publications izayamika kwambiri.
Mutha kulankhula ndi Vinjeru Ngwira pa 0995000036 kapena Dr Mwale pa 0991259788 komanso Nellie kumwenda pa 0983 69 29 00
www.avantmalawi.com
DR MWALE