Mukuluwiko ikupezeka lero mu kalata ya oBwande ndi iyi;
Chimseka pachimera
Kudya mtedza wachingonga
Kumangirana njoka m’masamba
Akapsala sagulitsana nkhwangwa yoduka
Kugwira ziputu
Achoka a malizagundu, tiyanike imswa
Zachoka ndundu tulutsani imswa
Bongololo ndi ndiwo timadya ndi auje
Kugona chimwini nsomba
M’manja mwabwinobwino
Kampeni kumphasa
Kuseweza Jere
Buluzi kuthandiza mbewa kuthawa
Bwezi ndi mtanthira, mulamba udaolotsa khoswe
Kuthiridwa madzi
Chamuna sayanika
Chamkuka nkhali ya Gaga
Timsomba ting’onoting’ono
Umagudulira.
Tithokoze nonse chifukwa chomvesera. Bwande Letters ndimakalata amene nthawi Zina amazukutidwa ndi ophunzira kusukulu za ukachenjede mdziko muno. Kangapo konse Bwande wakhala akuyitanidwa kusukulu za ukachenjede kukalankhulapo za kugwiritsa ntchito msinjiro za chilankhulo polumikizana ndi ena. Enjoy your Easter Monday
Share this article