MVULA YA MPHAVU YAGWA KU NKHATABAY

Pomwe nyengo ya mvula yayandikira zikusonyeza kuti mavuto angozi zakusefukira kwa madzi akhalaponso mdziko muno.

Lero mvula ya mphamvu yavumba kwambiri ku Tukombo mdera la mfumu yaikulu Zilakoma ku nkhatabay, mvulayi inayamba mmawa 5 koloko ndipo yasiya cha mma 8 koloko. kamba ka mvula yamphavuyi madzi asefukira ku chipatala cha Tukombo makamaka mu ma tent momwe amathandizira anthu odwala nthenda yakolera yomwe ikuvutabe muderali.

Avant publications inakayendera malowa ndipo yapeza kuti ma tent onse ali mmadzi ndipo odwala sangathandizikirenso mmalowa. Mfumu yaikulu zilakoma yapempha boma kuzera mwa nduna ya zaumoyo mayi khumbize kandondo chiponda kuti achite machawi pounikira za vutoli kamba koti odwala ambiri atha kusowekera thandizo loyenera zomwe zingaonjezere kufala kwa kolera mu derali.

Mfumuyi inapemphanso anthu kuti apilize kukhala a ukhondo kuti matendawa asafale monga pachiyambi.

Polankhula ndi Avant publications Mmodzi mwa a komiti yoona za ukhondo mderali a Barness Folo Mwale alangiza anthu onse mdera la mfumu zilakoma kuti akhale osamala kwambiri kamba koti nthenda ya kolera imafala kwambiri nthawi ya mvula ndipo pomwe mango ali mkati aliyense akhale ndi udindo osamalira moyo wake.

Tukombo ndi dela lotchuka kwambiri kumwera kwa boma la nkhataby ka usonzi ndi chakhalidwe.

www.avantmalawi.com

DR MWALE

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *