Nyumba ya malamulo lero yavomereza kukonzanso ena mwa malamulo okhuzana ndi katangale.
Mwa ena mwa malamulo omwe akufuna kusinthidwa ndi oti bungwe lothana ndi katangale mdziko muno la ACB lileke kufunsa chilolezo ku bungwe la director of public Persecution (DPP) .
Mmalawi muno bungwe la ACB likafuna kumanga munthu pa nkhani ya katangale limayenera lifunse kaye ku DPP, zomwe zimatsautsa kwambiri chifukwa milandu ikakhuza anthu oziwika director of public prosecution amakana kupereka chilolezo kuti anthu amenewo afufuzidwe.
Monga zakhalira matsiku angapo apitawa mdziko muno.
Izi zimaonetsa kuti nthambi ya DPP ndiyomwe imakolezera mchitidwe wakatangale popeza imatchinjiriza ochita mchitidwewu. Izi zinapangitsa amalawi ambiri kukhuzidwa komanso aphungu ena anyumba ya malamulo apereka pempho ku parliament kuti bwanji lamulo lopempha chilolezo ku DPP lichoke.
Pakadali pano aphungu onse agwilizana kuti lamulori lichoke ndipo tsopano ayamba kukambirana mfundo zoti zitsatilidwe kuti mpaka lamulori likhazikitsiwede. Lamulori likusiyana ndi loti president achepetse mphamvu zake ndipo musasokoneze.
www.avantmalawi.com
DR MWALE