Lero pa 21 june, President wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera ali ndi msonkhano wa atola nkhani, pamene Kwatsala mpindi zochepa kuti mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera alakhule mtundu wa Malawi nthawi ikamakwana 6 koloko madzulo ano.
Amalawi ambiri ali tcheru kufuna kumvera kuti chakwera alankhula zotani. chiyembekezo cha a Malawi chili chodzaza kufuna kumva mawu a mtsogoleriyu. a katswiri ena a ndale apempha a Malawi kudekha popeza zimene tsogoleriyu afuna kulankhula sizikudziwika.
Msonkhano wa president chakwera kwa atolankhani ukubwera pamene mu dziko muno mwachitika Nkhani zopatsa chidwi, monga kumangidwa kwa SUSU yemwe ndi mu China pomukayikira kuti amajambula monyazitsa kanema a Malawi mkumatumiza ku dziko la kwawo, Nalo bungwe lothana ndi ziphuphu la ACB linapereke lipoti la anthu omwe akukhuzidwa ndi katangale. masiku 21 amene mtsogoleri wa dziko anapereka ku bungwe la ACB pa nkhani zokhudza lipoti la Zunneth Sattar apita kumapeto ndipo ACB yakwanilitsa lonjezo la president. Komanso amalawi tisaiwale achakwera analonjeza mtundu wa amalawi kuti asintha kayendesedwe ka zinthu mmalawi muno pakutha kwa zaka ziwiri. Lero ndi ndendende zaka ziwiri kuchokera pomwe amalawi anavota pa 20 June 2020 kodi achakwera akufuna kutula pansi udindo? Mwina akufuna kutiuza za zomwe zili mu mgwiliriza wawo ndi a chilima?
Amalawi ali ndi mafunso ambiri koma kuti musaphonyane ndi izi tcherani kuti lanu pa avant publications kuti mumve zomwe a chakwera alankhule.
www.avantmalawi.com
DR MWALE