TSANGANO POLICE UNIT INAIWALIDWA

Anthu ambiri akamamva tsangano amaona ngati ndi malo ochitira malonda a kachewere omwe ali mmbali mwa msewu wa M1 ku Ntcheu. Koma zoona zake ndi zakuti apa ndipokhothera chabe kupita kutsangano kwenikweni komwe kumatchedwa kuti ku Ngoni. Ndipo kuchoka pa msewu wa M1 kukafika ku tsangano kungoni ndi mtunda okwana 75km.

Kumeneku ndikumalire a dziko la Malawi ndi Mozambique komwe kumachitika dzithu zosiyanasiyana. Boma linakhazikitsako polisi ngati mbali imodzi yokhwimitsira chitetezo cha mmalire mwa dziko.

Komatu nkhani yomvetsa chisoni ndiyokhumudwitsa ndiyakuti kumaloko zoti kuli police ndi dzina chabe. Inde tikuti boma linaiwala zoti kuli tsangano police unit. nyumba yomwe akugwiritsa ntchito ngati police ndiyochita kubwereka ku khonsolo, ndipo ndiyosalongosoka, nthawi ya mvula polisiyi simagwira ntchito kamba koti mumazaza madzi kukhala ngati muli panja kuli kudontha. Nyumbayi inagumukagumuka, zitseko zosalongosokanso , mipando yokhalira apolisi ndiyomvetsa
Chisoni kwambiri. Ukafika pa polisiyi ndi mlandu usayembekezere kuti akulemba statement kamba koti palibe chipangizo chilichonse chogwilitsa ntchito ngati pa polisi.

Avant publications inayendera polisiyi ndipo zomwe inaona ndizomvetsa chisoni kwambili. Anthu akuderali atafunsidwa za polisiyi anati ndi dzina chabe kuti tili ndi polisi koma ndizomvetsa chisoni kuti kumalire ngati kuno kuzikhala polisi ngati iyi. Tili kumalire ndi dziko la Mozambique komwe zauchifwamba sinkhani nde akaona chitetezo chathu chili chochepa amangotilowerera momwe akufunira, timaberedwa, mbewu zakumunda, katundu monga njinga zamoto ndi zina ndikumathawira ku Mozambique yatero nzika ina ku tsangano ku ngoni

Kunena zoona tilibe chitetezo chokwanira, polisi yonseyi tili ndi apolisi awiri okha nde mukuganiza anthu angagwire bwanji ntchito dera lalikuku ngati lino? Anatero mzibambo wina ochita malonda pa trading ya pa tsangano ngoni.

Avant publications inachita chidwi ndikukalowa mu polisiyi. Ndipo zinali zovetsa chisoni kuona apolisi awiri a sub inspector kayuni komanso Sargent Singanyama atangokhumata pa zimipando zophotchoka ziwili zomwe zili mkatimo akukambirana kuti atani ndi chigulu cha anthu omwe abwera panja kufuna chithandizo cha anthu awiriwa.

Titawafunsa a sub inspector kayuni anati ndizomvetsa chisoni kuti boma kuzera mu nthambi ya zachitetezo imaiwala kutimangira polisi yabwino kuno, malo anapezeka kale koma patenga zaka zochuluka kuchokera nthawiyo mpaka pano palibe chikuchitika, ntchito imatikulira kuno anthu awiri sitingapite mmudzi kukamanga anthu omwe apalamula pena timaopa chifukwa timatha kuchitidwa chipongwe. kukakhala mayeso a boma zimativuta timayenera titseke ofesi kuti tipite kumayeso ndipo kukachitika zovuta mwadzidzi timakasiyanso mayesowo ali mkati kuthamangira kuofesi. Zomwe zimaikanso pachiopsyezo mayeso aboma. Sizoona kuti polisi unit pazikhala apolisi awiri okha. Tikupempha akuluakuku a polisi komanso mabwana athu kuti atiganizire kuno kukufunika apolisi ambiri, zida zogwilira ntchito monga mapepala olembapo ma statement, komanso polisi yooneka bwino. Posachedwa kunabwera apolisi aku Mozambique kuzatiyendera ngati njira imodzi yolimbikitsira ubale wathu komanso kukhwimitsa chitetezo, tinachita manyazi kuti akhala pati ndipo tinajambulitsa zinthuzi zomwe zinatichititsa manyazi chifukwa panalibe chilichonse chozindikilitsa kuti ndi pa polisi.Watero sub inspector Kayuni.

Malingana ndi mtola nkhani wa avant publications, zomwe tinaona ku tsangano ngoni ndizokhumudwitsa ndipo kukukhala ngati sikumalawi. Kwakukulu tiyamikire apolisiwa popanga ubale wabwino ndi anthu komanso kugwira ntchito motamandika posatengera kuchepa kwawo

Tikupempha wankulu wa polisi bwana kainja kuti awauze assistance commissioner of police a ntcheu bwana munthali kuti apite akaone ndikukonza zinthu chifukwa chitetezo cha dziko chili pa chiopsyezo ntchito ikukula apolisi akuchepa. Angakhale apolisi awiliwa akuyesesa kugwira ntchito mozipereka koma anthu akuchuluka kwambiri okha sangakwanitse wonjezerani apolisi komanso mangani polisi yabwino kumaloku.

www.avantmalawi.com

DR MWALE

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *