BUNGWE LA WATERBOAD LIKUSOKONEZA CHITUKUKO CHA MISEWU

Chitukuko cha misewu ndi chofunika kwambiri ndipo mzika iliyonse imakondwera ngati misewu ili yabwino chifukwa mayendedwe amakhala abwino komanso ntchito za malonda zimayenda bwino koma anthu akudandaula ndi zomwe bungwe la waterboad likuchita pozakumba msewu womwe wangokonzedwa kumene.

Chomwe chimachitika ndi chakuti anthu akadandaula ku boma kuti awakonzere nsewu womwe wakhala nthawi yaitali. Zimatenga nthawi kuti izi zichitike, koma msewuwo ukangokonzedwa posakhalitsa ma kontilakitala a bungwe lolumikiza madziwa amabwera ndikuzagumulanso msewu wanyuwaniwo ndikumagwilapo ntchito yawo.

Ena mwa malo amene akumbidwa ndi okonza madzi ku area 49, nsewu wa guliver

Izi zikudabwitsa anthu mdziko muno kuti bungweli likupangiranji zimenezi? Nanga nthawi yomwe msewu usanakonzedwe bwanji sakumachitiratu izi? Kapena akaona kuti msewu ukuyamba kukonzedwa chifukwa chani samapita kukaoneratu mapayipi awo? Chowawa kwambiri komanso chokhumudwitsa ndichakuti akagumula msewuwo amangokwilirapo ndi donthi basi nkumapita zomwe zimapangitsa boma kuti lizalembenso kontilakitala wina kuti akonze msewu omwewo. Izi zapangitsa anthu kuganiza kuti izi zikumachitika mwa dala ndicholinga choti ndalama za boma zizionongeka mnjira imeneyi .

Izi sikuti ndi nkhamba kamwa ayi avant publications inachita chidwi ndi zomwe zachitika ku area 49 Guliva komwe msewu wakhala nthawi osakonzedwa ndipo chongoumaliza kukonza bungwe la water board lakumba msewuwu m’mbali monse zomwe zikunyasitsa tchito yobwino yomwe boma lagwira. Nzika ina yaku guliva yati msewu uwu ukangokonzedwa a waterboad satenga nthawi kubwera kuzagumula koma sabwezeretsapo mmene panalili. Apatu titha kunena kuti wina akakonza wina amabwera kuzaononga.

Ndizoonadi ukamapanga chitukuko zina zimaonongeka koma khalidwe ili silabwimo mukapanga ntchiyo yanuyo bwezeretsani mmene panalili ikaninso tala monga anaikira anzanu tikatero chitukuko chiyenda bwino.

Avant publications ikupempha bungwe la waterboard ndi ena onse omwe akupanga ntchito yawo pa nsewu kuti akumbukire kupezanso kontilakita ozaika tala malo omwe agumulawo kuti chitukuko chipitilire. Izi sizikuchitika ku lilongwe ku guliva kokha ayi koma dziko lonse la malawi. Chonde sinthani khalidweli mukuononga chitukuko.

www.avantmalawi.com

DR MWALE

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *