“Lolani ntchito za manja anga zindichitire umboni” awa ndi mawu omwe tingakumbukire pulezidenti wachitatu wa dziko lino malemu Bingu Wa Mthalika yemwe anamwalira zaka khumi zapitazo pa 5 April 2012 atangogwa mu ofesi kamba ka nthenda ya mtima.
Akubanja kwa a mthalika akonza mwambo wa ma pemphero okumbukira malemuwa omwe ukachitikire ku tchalitchi cha chingazi kwa goliati ku thyolo, ndipo mwambo woika nkhata ukachitika akatha mapempherowo ku ndata farm (mpumulo wa Bata) komwe a Bingu anaikidwa.
Amalawi ambiri amawakumbukira president Bingu wa mthalika ngati president yemwe anachita zitukuko zambiri zomangamanga mmalawi muno. Iye anamanga parliament, Bingu stadium,sukulu ya ukachenjede ya MUST,,msewu wa chipembere highway, komanso chitipa – Karonga road. Komanso anali president oyamba kubweretsa ndindomeko ya sabuside yomwe inathetseratu njala m’dziko muno.
Zabwino zili apo panalinso zofooka zake zomwe zinapangitsa kuti anthu amuukire kuchita zionetsero dziko lonse, monga kusowa kwa mafuta komanso ulamuluro omwe amati unali omva zake zokha.
Mwambo okumbukira malemu Bingu wachitika koyamba chimwalirireni angakhale kuti mchimwene wake ndi yemwe a
Wakhala akulamula kwa zaka zisanu ndi chimodzi.
Muuse mu mtendere a Bingu
www.avantmalawi.com
*DR MWALE*