A mfumu a yiteta komanso anthu ena anayi a m’boma la Rumphi amangidwa kamba kophwasula nyumba zokwana zinayi za banja la a chawinga kamba kowaganizira kuti ndi a mfiti.
Malingana ndi mneneri wapolisi ku Rumphi sajenti Tupeliwe kabwilo wati anthuwa anamangidwa pa 15 march 2022 pomwe apolisi a zofufuza anapita kumalowo kukafufuza za nkhaniyi ku hewe.
Mabanja awiriwa akhala akukangana pa nkhani ya malo ndipo mwazizi banja linalo kunamwalira munthu pa 2 march ndipo a mfumu a yiteta anazuzula anthu a ku banja la chawinga kamba ka imfayi ponena kuti ndiwo aloza munthuyo zomwe zimapangitsa kuti abale a munthu omwalirayo akagumule ma nyumba a ku banja la chawinga komanso kuononga katundu
Anthuwo ndi a penston chawinga 62, a mmundzi mwa yiteta, sanudi ng’ambi 48, kenani ng’ambi onse a zaka 33 ndipo ama chokera mmudzi mwa masilira , a Lezawawa ng’ambi 42 a mmudzi mwa chalowalowa ndi a Catherine ng’ambi a mmudzi mwa kasalika ndipo onse a mundzi mwa mmfumu yaikulu katumbu ku Rumphi komweko.
www.avantmalawi.com
DR MWALE