Mabanja 117 akusowa pokhala ku ndirande

Mabanja 117 ndiwo anakhudzidwa ndi ngozi ya madzi osefukira ndinso mphepo ya mphamvu yomwe inakhudza dera la Ndirande munzinda wa Blantyre pa 4 January chaka chino.

Malingana ndi lipoti la nthambi yowona ngozi zogwa mwadzidzidzi ku khonsolo ya nzinda wa Blantyre, ngoziyi inakhudza madera a makhansala atatu omwe ndi Makata, Matope ndi Gamulani.

Lipotili latinso, anthu khumi ndiwo anavulala ndipo palibe yemwe anamwalira komanso malonda a anthu makumi awiri anawonongeka omwe ndi a ndalama pafupifupi K20 million.

Nyumba zokwana 115 zinawonongeka denga pomwe ziwiri zinagweratu kupangitsa kuti eni ake asowe pokhala.

Pangoziyi, mpanda wa sukulu ya pulayimale ya Makata unagwa.

Follow avantmalawi.com

Share this article

One thought on “Mabanja 117 akusowa pokhala ku ndirande

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *