Ku M’mawaku, Mayi Gotani Hara ngati olankhulira nyumba ya Malamulo anamema ophunzira amene akukonzekera kulemba mayeso a Std 8, Folomu 2 komanso folomu 4 kulimbikira mu chaka chikubwerachi pakuti iwo ndi atsogoleri a mmawa.
A Hara analankula mawuwa pamwambo wapadera umene amasangala ndi nyamata wa zaka khumi ndi zitatu, yemwe wakhonza bwino mu mayeso a ku Pulayimale a mu chaka cha 2023.
Henderson Levison amene wasakhidwira ku Dedza Secondary school anakaonekera ku nyumba ya malamulo, ndipo aphungu onse anali okondwa ndikumulimbikitsa. Nyamatayu amaphunzira pa pulayimale ya Nampeya mu boma la Machinga.
Mwa ophunzira ena omwe achita bwino ndi Chulu Alinafe, yemwe maphunzira ku Playdor ku Blantyre. Mbewe Angel, amene amaphunzira ku mphongole ku Kasungu komanso Ngosi Wakisa wa ku Nzimba, Ekwendeni.
Zambiri tsatani Avantmalawi.com