olemba Dr Mwale
Pafupi fupi masabata awiri tsopano anthu aku nkhatabay South akhala akudabwa ndi kudwala kwa anthu mwa dzidzidzi. Zomwe zikuchititsa mantha anthu okhala muderali.
Mosaziwika bwino anthu akhala akutsegula mmimba mododometsa komanso kusanza kosalekeza ndipo kenako ndikufooka nthawi yomweyo. Izi zikuchitika kwambiri ku tukombo kwafumu yaikulu Zilakoma.
Avant publications inachita chidwi ndi nkhaniyi ndipo yafunsa nzika zakuderali zomwe zikuonetsa kukhuzika kwambiri ndi nthendayi, modzi mwa anthu omwe avant publications yalankhula nawo a Frank Zoto ati chomwe chikukhuza kwambiri ndi choti poyamba anthu ankaganiza kuti ndi cholera koma azachipatala anakana kuti iyi sikorera, izi zikudetsa nkhawa chifukwa anthu sakudziwa kuti kweni kweni awa ndi matenda anji ndipo thandizo lake ndi lotani.
Chiyambireni nthendayi anthu okwana anayi amwalira mderali ndipo tsiku ndi tsiku anthu akutumizidwa kuchipatala chachikulu cha chintheche komanso nkhatabay.
Mderali muli chipatala cha boma chaching’ono chomwe sichikukwanitsa kupereka nthandizo loyenera pa matendawa kotero kuti anthu ambiri akudzanana pa chipatala cha private chomwe malingana ndi a Franck zoto ati nako kwazaziratu.
Avant publications ikupempha nduna yoona za umoyo a Khumbize kandodo chiponda kuti achite machawi potumiza akatswiri a zoyeza matenda kuti akaone chomwe chikuchitika. Pakadali pano anthu aganiza zomanga msasa oti anthu odwala azigonekedwapo pachipatalapo.
Malingana ndi anthu ena omwe Avant yacheza nawo iwo akuti anthu ena akukumba golide kuntunda kwa derali zomwe zikupangitsa kuti madzi azikhala okuda nthawi zonse, kamba kosowa madzi a ukhondo malingana ndi kuchepa kwa mijigo anthuwa amakakamizika kugwilitsa ntchito madziwa pa ntchito zina za pakhomo ndipo izi zikupereka chiopsyezo kwa anthu a mderali.
komabe angakhale izi zili chomwechi pali Madera monga kuwiri, chapeta komanso kuntunda kwadera la kande nakonso nthendayi yabuka.
Mfumu yaikulu zilakoma ndi anthu ake mderali akupempha boma kuti lichitepo kanthu msanga vutoli lisanafike poipa.
*DR MWALE*
www.avantmalawi.com
Oooh zovuta kwambir
Tavisuska ukongwa