Kunali Chimwemwe Ku Nsanje North, Mdera lotchedwa Chambuluka pamene a ESCOM pansi pa utsogoleri wa Dr Lazarus Chakwera anapita kukadzala Transformer.
Delari liri mu Constituency imene kukuchitika chisankho cha chibwereza, chomwe a Esther Mcheka Chilenje a DPP anachotsedwa pampando ngati MP ndi Court. Pomwe a Enock Chizuzu a MCP analumira mulomo kukanitsitsa kuti chisankho sichinayende bwino.

Litagamula Khothi lalikulu ku Blantyre kuti chisankho chachibwereza chichitikeso pa 30 March, 2021. Kuli kalikiliki andale kupangitsa kampeni, pamene tikuona a ndale osiyana siyana kumema anthu kuti awavotere.
Izi zili Choncho, a Enock Chizuzu omwe ndi a MCP anamema a boma kuti abweretse chitukuko cha Transformer chomwe mnzika za Mdelari zakhala zikuvutika kwa zaka.
Ngakhale m’mbuyomu a Chilenje ayesesa kupempha chitukukochi chomwe chimalowa ma million ochuluka, sizinaphule kanthu. Koma kulowa boma la mgwilizano wa Tonse kuzera mwa phungu oyimira MCP a Enock chizuzu sanazengereze koma kupereka chitukuko chomwe anthu akhala akuchiyembekezera.
Koma kubwera kwa magetsiwa zatengera luntha la phunguyu ndipo waonetsa chamuna chake pamene usiku wa lero anthu a Mdera la Chambuluka ku Nsanje agona mowala chifukwa cha magetsi amene a ESCOM awayikira
Polankhula ndi a Chizuzu, iwo apempha anthu a mderali kuti awavotere kuti apitilize kupereka chitukuko monga ichi ndi zina. Achizuzu ati iwo ndi mtumiki anthu amene abweretse chitukuko kusiyana ndi a Chilenje omwe amangolonjeza koma osakwaniritsa.
A Chizuzu ati ubale wawo ndi a President a Chakwera ndi wa Mtengo wapatali, umene ubweretse chitukuko mu derali ngati awavotere kukhala MP pa 30 March pano.
Nawo anthu amderali Polankhula ndi Avant ati ndiokon dwa kwambiri ndi zomwe wachita chizuzu kamba koti waonetsa kuti ali ndi mtima ofuna kutukula dera lake osati kungozikundikira yekha ndipo iwo alonjeza kumuvotera pa 30 March pakubwerapa
www.avantmalawi.com
*DR MWALE*