NGONGOLE YA NEEF(MARDEF)

by Dr mwale

Boma la Malawi linapeza ndalama zochuluka zokwana 75 billion zomwe cholinga chake ndikubwereketsa anthu kuti ayambe ma business osiyanasiyana izi zikuchitika ndi cholinga chofuna kukwaniritsa mfundo za boma la Tonse kuti amalawi azikhala ozidalira pa chuma komanso pa chakudya, iwo akuti anthu ngati ali ndi ndalama ndekuti chakudya ali nacho zomwe zikuthandauza kuti atha kumadya katatu pa tsiku. Komanso akufuna kukwaniritsa mfundo yolemba anthu 1millin ntchito.

Zofunika kuchita kuti upeze ngongole

Ulendo uno sizomalembana mwanseli ayi ,palibe zachinyezongo apa ,ngati mukufuna ngongole pangani gulu lanu la anthu 10 ndipo lipatseni dzina lake. mukhale anthu oti nonse mukukhukulupirirana kuti palibe azavute kubweza ngongole. Sankhanani ma udindo anu monga chairman, secretary ndi treasure, .

Lembani dzina la membala aliyense, foni nambala yake, nambala ya chiphaso Cha unzika komanso kumapeto kwake ikaniko ndalama zomwe munthu akufuna kuzabwereka. Pangani fotokope zipanso zanu zonse 10 zikhale pa pepala limodzi. Pangani malamulo a gulu nawo akhale pa pepala lake. Mapepala onse akwane atatu,(choyamba Cha maina ndi ndalama zomwe mufuna kutenga, Cha malamulo ndi Cha ma ID)

Kodi mutha kubwereka ndalama zingati

Malingana khumbo la boma amafuna kuti munthu aliyense atengepo ndalama yomwe angazakwanitse kubweza kuthandauza kuti palibe malire, komanso kamba ka kuchuluka kwa magulu omwe akupangidwa boma kudzera mwa NEEF akhazikitsa kuti gulu lililonse likuyenera kuzalandira ndalama zokwana 5 million zomwe zikuthandauza kuti aliyense ali ndi ufulu otenga ndalama zokwana 500,000. Ngati paguku lanu anthu akutuna kutenga ndalama zochepa wina Ali ndi ufulu kutenga ndalama zochuluka kuposa 500,000 koma bola kubweza komanso bola ndalama zonse pa gulupo zisadutae mlingo wa 5 million.

Ndalamayi ndiyobweza zaka zingati?

Malingana ndi kafukufuku yemwe Avant publications yapeza zikuoneka kuti boma likufuna anthu akhale ndi ndamala mnthumba mwawo osati awapatse phuma pobweza choncho boma laika kuti ngongoleyi ibwezedwe kwa zaka zitatu zomwe zikuthandauza kuti aliyense yemwe watenga 500,000 azizabweza ndalama yokwana 14,200 pa mwezi ulionse.

Kodi Pali chiongola dzanja?

Ndalamayi ndi ya boma kuthandauza kuti ndi yanu yomwe nde boma laika 5.2% kwa azibambo komanso 2.5% kwa azimayi. Malingana ndi Avant tapeza kuti munthu akabwereka 500,000 ndalama pamwamba ndi 27500 pa zaka zitatu.

Pangani ma gulu azibambo,azimayi komanso achinyamata ndipo funsani akhansala akwanu kuti akulozereni kokapereka zikalata zanu.

Mukapanga ndikukapereka kuzabwera mlangizi yemwe azaphunzitse magulu onse omwe mwapanga za mmene ngongoleri izayendere ndipo mlangizi ameneyu ndi amene azabwere ndi ma fomu a NEEF obwe muzasaine, musapusisidwe kuti wina akubweretsa fomu mmudzi nkumati ndi ya NEEF akuberani ulele.

Ngati simunapange gulu iwalani kuti mupeza ngongole, ndipo musadikire anzanu koma khalani anthu okwana ten ndikutsatira zomwe ndanenazi.

www.avantmalawi.com

DR MWALE

Share this article

4 thoughts on “NGONGOLE YA NEEF(MARDEF)

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *