THE MATTER IS IN COURT
Bwalo la milandu ku balaka laimisanso mulanduwu omwe a Rose matewere komanso ana awo akuwazenga ovulaza mzimayi
Sabata yatha mulanduwu unaimitsidwa kuti uzapitilizidwa lero , koma tikunena pano mulanduwu waimitsidwanso, avant publications itafunsa
mulembi wa bwaloli a Gladys Gondwe kuti chikuchitika ndi chani kuti mulanduwu uziyimitsidwa? iwo apempha nthawi yokwanira kuti afufuze kuti mulanduwu ukuyenda bwanji komanso kupeza chomwe chikuchitika kuti aziuimitsa. Pakadali pano Anthu atatuwa akuwasunga ku ndende ya ntcheu.
Mayi matewere ndi ana awo awiri akuwazenga mulandu ovula ,kumenya komanso kunyazitsa mzimayi zomwe zinachitika kumayambiriro a mwezi uno
Amene mukukumbukira bwino, mayiyu anawoneka mu kanema imene idali yonyazitsa komanso yopereka mafunso ku Chikhalidwe chathu cha Chi Malawi. Mukanemayu ena ankafotokoza kuti Mzimai amene amkamenyedwayu anali pa unwenzi wa nseri ndi mamuna wa mayi matewere.
Kotero Mayi matewere ndi ana ake anakonza chipongwe kudikira Mzimayi winayu pansewu pamene adamumenya ndi kumuvula zovala za mnthupi.
Pakuti nkhaniyi ili ku court sitikambapo zambiri koma kudikira timve zotsatira za ku court
www.avantmalawi.com
DR MWALE