MBAVA YOOPSA YOBA MA BATILE A GALIMOTO YAWONA ZOOPSA

Mbava mukuyionayi yawona zoopsa pamene imafuna kuti ikabe ma Batile a Galimoto

Nkhaniyi ikuti..Bambo Kathumba omwe amakhala ku Chikwawa boma pa Trading Centre dzuro usiku ndi akazi awo adapita ku Party yomwe imachitikila pa Nchalo yomwe nzawo adawayitana.

Ndipo ku Nyumba kwawo adangosiyako ana awo ndipo Mbavayi idapezerapo mwayi oti ithe kuba pa Khomopa.

Koma la 40 likakwana Mbavayi akuti adakwanitsa kutsekula Galimoto koma atangogwira Batile nthawi yomweyo Manja ake adakakamila ndipo adayesesa kuti achotse mpaka adayamba kulira momvetsa chisoni zomwe zidapangitsa anthu ena oyandikana ndi Nyumba ya a Bambo Kathumba kuti athamangile ku Mpandako akawone chomwe chimachitika ndipo apa ndipamene adayipeza Mbavayi ikutulutsa Misozi yosamba uku akuti ndaleka kuba.

Mwini Nyumbayi adayimbilidwa Foni ndipo adafika ndikuwaza Mankhwala Mbavayi ndipo idagwa pansi komanso kudabwa kuti wachotsedwadi mmanja katundu yemwe adabayo.

Ndipo Mbavayi ayitengera ku Police ya Chikwawa.

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *