Monga mphekesera zakhala zikumveka masiku apitawo kuti Katswiri wakale wa team ya Silver Strikers, Khuda Muyaba wasayina ndi timu ya ku Syria.
Lero titha kutsikimiza kuti Khuda Muyaba akhala akusewera ndi timu ya Tishreen sporting club, yomwe imapezeka mu nzinda wa Lattikia ku Syria.
Tishreen ndi timu yayikulu komanso yakale kwambiri ku Syria. Timuyi yatengapo ukatswiri wa Syria club kopitirira ka Khumi.
Tishreen club inayamba mu 1947 ndipo Stadium yake yapakhomo imatchuka ndi dzina loti Al-Assad.
Khuda Muyaba akhala katswiri oyamba kukasewera ku dzikoli ndipo izi zatseka mano ng’ononong’o onse akhala akumveka kuti katswiriyu akufunidwa ndi a Mighty Mukuru Wanderers komanso a chitipa United.
Khuda azilandira ndalama zokwana K1,700,000 zimene zili USD 1,700. Ubale osewera ku Tishreen ndi wa chaka chimodzi umene uzathe pa 9 may 2024. Ndipo ndi wa ndalama zokwana USD 20,000 Zimene zili K21.7 million ku Malawi kuno.
Zambiri tsatani avantmalawi.com