Kwatha kwa lero, Chitipa United yaona mbonaona pamene Clement Nyondo wagoletsa chigoli chomwe Dedza Dynamos yapambanira pa Dedza Stadium. Nyondo padakali pano palibe wotsutsana naye pamene Ali ndi zigoli zochuluka mu Tnm SuperLeague.
Nako ku Kamuzu Stadium, ma palestina a Nyasa Big bullets amwa wamkaka pamene athyola nthiti za Extreme FC ndi zigoli zitatu kwa chilowere. Bullets tsono ili ndi ma points 34 kutenga umwini wa Tnm SuperLeague pamene ili pa nambala yoyamba kutsatidwa ndi ma Bankers omwe ali Ali ndi 32 points. Patrick Mwaungulu ndi amene wasakhidwa osewera wapamwamba ku Blantyre.

Nako ku Balaka stadium, ma Bankers awona mbonawona atagonja kwa Asilikali a Red Lions ku chigoli chimodzi kwa iyayi. Izi zapangitsa Silver Strikers kuchoka pa nambala yapamwamba mkufika pa nambala yachiwiri mu Tnm SuperLeague.
Kwalero mu sabata la nambala 17 titha kutsimikiza kuti Bullets ndi akatswiri a Tnm SuperLeague ndipo palibe angatsutse.

Zambiri tikupatsirani pa AvantSportsDesk