Nkhani ya Katemera wa covid19 yadzetsa manong’onong’o mdziko muno ponena kuti katemerayi ndioyipa mnthupi mwa munthu.
Koma malingana ndi president wa dziko lino a Lazarus Chakwera afuna kuonetsa anthu kuti zonse zomwe akhala akulankhula anthuwa ndi zabodza ndipo iwo sangaitanitse zinthu zomwe zingazaononge moyo wa anthu ake.pachifukwa ichi iwo ndi akazi awo a madam Monicca Chakwera onse alandira Katemerayi ku nyumba ya chifumu lero ku zomba mmene nthawi imakwana 12:25 masana.
Avant publications yagwira mawu a nduna ya zaumoyo a khumbidze kandodo chiponda komanso a president a dziko lino kuti *Katemerayi siokakamiza amene akufuna akalandire komanso ngati sukufuna siya*
Mmene izi zimachitika nkuti wachiwiri kwa president wa dziko a Saulosi Chilima akulandiranso katemera yemweyu ku mzuzu.
Katemerayi azilabayidwa kawiri ndipo kachiwiri azabayidwa pakati pa masabata asanu ndi atatu ndi masabata khumi ndi awiri.
Pa mwambowu achakwera anaitana atsogoleri onse opuma mdziko muno monga a Bakili Muluzi, Peter Mthalika komanso mayi Joyce Banda kuti nawo akakhale mgulu loyamba kulandi koma wabwerako ndi Joice Banda yekha
Dziwani kuti mukabaidwa Katemerayi sikuti simungadwale matenda a covid19 koma kuti mukhale otetezeka ndipo simukuyenera kusiya kutsatira njira zozitetezera kupewa kachilomboka.
www.avantmalawi.com
*DR MWALE*