ADAYAMBANA CHANI UKRAINE NDI RUSSIA?

Kale kale kwambiri maiko ambiri anali pansi pa ulamuliro a wa maiko ena ndipo panthawiyo dziko la Ukraine linali pansi pa ilamuliro wa Russia pakuti maiko awiriwa anapanga malire. nthawi yomweyo nkuti Russia lili dziko lalikulu ndipo linkhatchedwa kuti USSR kapena kuti (EMPIRE) ndipo ukraine inali mu USSR’s ngati dziko limodzi.

Ku mpoto kwa Europe kunabadwa mugwiliza wa maiko omwe amautcha kuti North Atlantic Treaty Organization (NATO).

kamba koti panali kusagwilizana kuyambira pachiyambi pakati pa maiko aku mpoto kwa Europe ndi dziko la USSR lomwe lero ndi Russia, maikowo saoneranabe kukondwa mpaka lero.

Nde zaka za mmbuyomu dziko la Ukraine linaonetsa chidwi cholowa mu NATO ndipo maganizo awa sanasangalatse Russia poganizira kuti Ukraine ikalowa NATO ndekuti ikhala ndi mdani yemwe ndi neba ndipo maiko onse amu NATO azathakuzagonjetsa Russia polowera mu Ukraine.

President wa ku Russia wakhala akuchenjeza komanso akukambirana ndi Ukraine kuti asapange izi Popeza iwo anali pa ubale wawo kuyambira kale

Koma president waku Ukraine amakana kumvera izi kamba koti nthawi zambiri Russia imachita mtopola ofunakulowerera malo ake ndikulanda madera awo ena.

Nkhaniyi sinaphure kanthu kamba koti president waku Ukraine anapempha joe Biden kumayambiriro a 2021 kuti dziko lawo lilowe nawo mu NATO zomwe zinathekadi. Chifukwa Ukraine imadziwa kuti ikalowa mu NATO Russia iwopa singapange nawo mtopola poti mu NATO muli maiko a nkhondo mphamvu komanso ambiri.

A Ukrainian serviceman fires his weapon during an exercise in the Joint Forces Operation, in the Donetsk region, eastern Ukraine, Tuesday, Feb. 15, 2022. While the U.S. warns that Russia could invade Ukraine any day, the drumbeat of war is all but unheard in Moscow, where pundits and ordinary people alike don’t expect President Vladimir Putin to launch an attack on its ex-Soviet neighbor. (AP Photo/Vadim Ghirda)

Russia ikuthira nkhondo ku Ukraine ndicholinga choti ichoke mu NATO komanso pofuna kukakamiza NATO kuti isalowere maiko akumvuma kwa Europe komwe Russia ili ndi mphamvu.

Ndipo pakadali pano Russia ikunena kuti maiko onse akuzambwe kwa Europe avomereze kuti NATO isachite za nkhondo kapena training kumvuma kwa Europe kuphatikazo ku Ukraine

Izitu zikuthandauza kuti Russia ikufuna izilamulabe Ukraine ndipo imafunitsitsa italanda likulu la Ukraine lomwe ndi Kyiv.

Titsatileni pa www.avantmalawi.com

DR MWALE

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *