A police amanga Raffick Issa wa zaka 29 kamba kogwilira mtsikana wa zaka 15, izi zatsimikizidwa ndi wofalitsa nkhani wapa police yaku kawale.
Mtsikanayu ali form 1 pa sukulu ina mu mzindawu, ndipo chomwe chidachitika ndi choti Aunt ake a mtsikanayu adamutuma kuti akatenge sukulu uniform ya mchemwali wake yomwe adapatsa telalayu kuti asoke.
Mtsikanayu adafotokoza kuti telelayu yemwe ndi woyandikana Ndi nyumba yawo adamutuma kuti akagule chips ndi zinthu zina ku msika womwe uli pafupi, koma akubwelera kudayamba kugwa mvula yambiri zomwe zidapangitsa kuti mtsikanayu abisale nawo kaye nyumba mwa telalayu asadapite kwawo.
Telalayu kamba ka izi adapezelapo mwayi mpaka kumugwilira mtsikanayu. Mtsikanayu atapita kwawo adawuza izi abale ake omwe adakadandaula kwa amfumu omwe adayitanitsa a police kudzamanga telelayu. Pakali pano iye akuyembekezela kukawonekera ku court kuti akayankhe mlandu ogwilira mtsikana wa chichepele
*Avant Publication*