A MALAWI ASANKHE MWA NZERU.

Ma ola ochepa ndi omwe atsala kuti anthu avotere Pulezidenti wadziko lino, komanso phungu ndi khansala wa dera lawo. Pamene campaign yatsekedwa 6 koloko mmawa wa pa 14 September 2025, ife a Avant Publications mpamene tiyambe kupereka ma update mwa kathithi okhudza zisankho.

Miyezi iwiri yapitayi sitidakhale ndi danga lolemba kwambiri zokhudza ma campaign a zipani chifukwa pakati pa 2018 – 2020 anthu a ndale adatipatsa phunziro lalikulu kuti olo utawafera iwo amayendera mwambi okuti ndiolotse nkakutafune. Ngakhale Bon Kalindo mukulankhula kwake anati Malawi si omufera amakusiya iwe uzifa. Nchifukwaso tidasankha ngati avantmalawi kusatenga mbali mu ndale.

Tsono ife tigwira ndi Malawi Electoral Commission pofuna kudziwitsa tsatane tsatane wa mmene zisankho zikuyendera potengera kuti Nzika iliyonse ili ndi ufulu osankha mtsogoleri wa ku mtima komanso ufulu okhala ndi uthenga olondora.

Chikuchitika mchani pakadali pano ndi MEC?
Bungwe la zisankho lakwanitsa kugawa ma Presiding officers, Biometric Voter identification Clerk (BVIC’s) komanso security Officers mma tally centres komanso polling centres onse.

Mmawa pa 15 ma presiding officers akhale akuphunzitsa ma polling staff ntchito yawo, komanso ma observers ndi oyimilira zipani akhale akupanga check ma ballot papers amene tikunena pano afika kale mma tally centres.

Lachiwiri ikamati 6 koloko mmawa tizizalandilidwa bwino ndi Ma polling staff, kenako chiphaso chathu chizizalowa mu kauni ngatidi chili chovomelezeka, zikatero tizizapasidwa ballot paper mkuvika chala mu ink kupita kukavotera atsogoleri athu monga mwa nthawi zonse.

Zambiri tikupatsirani khalani pompo.

Avant Publications

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *