OGWIRA NTCHITO PA CHIPATALA CHA PA MONKEY BAY ANYANYALA NTCHITO

Anthu aku monkey bay anagwira njakata lero pomwe kuchipatala chawo Cha monkey community kunalibe thandi zolero .

Ogwira ntchito kumeneku akuti akufuna akulu akulu apachipatalachi awachotse ntchito kapena awasinthe ma udindo kamba koti asokoneza ndapama za covid19.

Malingana ndi anthuwa akuti pachipatalapa Pali anthu atatu omwe maina awo ndi a Mr Ndawa, Mr chaona komanso a kanthiti , anthu atatuwa akuwazuzula kuti anasokoneza ndalam za covid19 ndipo anzawo samawapatsa ma alawansi. Komanso atatuwa ali khalidwe lopondereza anzawo ndiposafuna kuti anzawo akwezedwe kapena achite zabwino.

Malingana ndi mmodzi mwa ogwira ntchitowa yemwe sitimutchula dzina pa zifukwa wati atopa ndi khalidwe la anthu atatuwa ndipo tsopano zafika pa mwana wakana phala.

Izi zasokoneza anthu kulandira thandizo la mankhwala ndipo mabwana apachipatalachi komanso anduna a zaumoyo chitanipo kanthu msanga.

DR MWALE

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *