MUNTHU ALAMULIDWA KUTI AKHALE M’NDENDE MIYEZI 18 CHIFUKWA CHOKHALA NDI CHIPHASO CHA MSCE CHABODZA

Bwalo lamilandu la First Grade Magistrate ku Phalombe lalamula bambo wina wazaka 24 kuti akakhale kundende chaka chimodzi ndi theka chifukwa chonamizira munthu yemwe watchulidwa mchiphaso.

Woyimira milandu wa apolisi Sergeant Maureen Namainja, adauza khotilo kuti woweruzayo, Alfred Twaya adapereka kwa Malawi Police Service, satifiketi ya MSCE ya munthu womwalirayo, pomwe amafunsira ntchito ya u-constable, mwezi watha.

Anamangidwa ku polisi ya Phalombe apolisi ena atazindikira kuti dzina la yemwe anali ndi satifiketi lidakonzedwa pogwiritsa ntchito tippex.

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *