olemba DR MWALE
Kumwera kwa boma la nkhatabay komwe phungu wake ndi olemekezeka a Ken zikhale ng’oma kwakhala kulibe police station chibadwireni Cha dziko la Malawi.
Anthu akuderali akumayenda mtunda wa utali kupita ku chintheche komwe kuli police, izi zikukoledzera mchitidwe wa uchifwamba, kuba komanso nkhaza zosiyanasiyana siyana kamba koti anthu oterewa amadziwa kuti sangawapititse kukikonse poti police ili kutali.
Kuchokera pa kamwala bridge kufika pa Dwambazi bridge ndi mtunda okwana pafupifupi 60Km koma palibe police station tangoganizani mavuto omwe ali mderali,
Nkhatabay constituency yakhalapo ndi aphungu monga Sam kadondo Banda yemwe kwawo ndi ku kande iwowa alamulirapo zaka khumi koma osabweresako polisi station, Aleke Banda yemwe ndi mmodzi mwa anthu oziwika pa nkhani yobweretsa ufulu komanso ulamuliro wa demokalase komaso wa zipani zambiri naye analamulirako kwa zaka zisanu(mzimu wawo uwuse mutendere) koma nawo sanabweretse polisi station, a Eta Banda nawo analamulako zaka zawo zisanu osabweretsa polisi station, a Emily chinthu Banda nawo alamulako zaka zisanu koma nawo alephera kubweresa polisi station. Pano kuli a zikhale ng’oma Kodi iwowa abweretsa police station kapena nawo angochoka?
Mderali muli mafumu akulu akulu (TA) awiri omwe ndi a fuka mapiri 7 omwe amakhala ku kande komanso a Zilakoma omwe amakhala ku Tukombo.
Derali muli ma court awiri omwe Ali ku kande ndi ku Tukombo koma ma court onsewa alibe ma majesitiliti oti atha kumazenga milandu moti oweruzawa amachita ku choka ku chintheche mu nthawi yomwe iwo afuna. Zikana khala Cha nzeru boma kuikanso ma polisi station ku malo omwe kuli ma khoti kale (Tukombo ndi kande) ndikutumizako oweruza milandu chifukwa zonse zitha kumachitika malo omwewa monga kumanga komaso kugamula anthu omwe apalamula
malingana ndi kafukufuku yemwe Avant Publications yapeza zikuonetsa kuti Kuchoka chintheche kufika pa kasitu muboma la nkhotakota pomwe Pali polisi ina ndi mtunda okwana ma kilomita pafupifupi 100 Kodi apa tingapewe bwanji mchitidwe wakuba,kupha komanso nkhaza kwa Ana ndi azimayi?
Anthu a mdera la nkhatabay south constituency akupempha boma kuzera mwa phungu wawo zikhale Ng’oma kuti aganizire zoika mapolice station kuderali makamaka ku kande ndi Tukombo.
www.avantmalawi.com