Olemba dr mwale
Anjinga za kabaza awombana pa Kona yapa chipasula, ndipo mmodzi wafera pompo.
Mmene nthawi imakwana 11:45 usiku wakabaza wina amachokera ku 23 ndipo wina amachokera ku Nchesi ,anthu onsewa amathamanga kwambiri moti yemwe amachokera kuchensi analephera kuyenda mbali yake pomwe amafuna kuti akhote pa Kona imeneyi ndipo anakaombana ndi mzake yemwe amayenda ku mbali yake.
Wakunchesiyu wafera pompo moti sanalakhulenso ndi mawu amodzi omwee koma sakudziwika kuti dzina lake ndani koma winayo anakwanitsa kulankhula koma wangoti ndi chisomo ndipo amayenda ku ranki yaku 24
Avant publication inafika mochedwa pa malopo moti inalephera kutenga zithunzi koma malingana ndi Mr magombo omwe analipo panthawiyi akuti ngoziyi yachitika kamba ka kuthamangitsa njinga kwambiri zomwe sizikufunika kutero potengera kuti pamalopa Pali Kona yoopsya kwambiri ndipo aliyense akuyenera kusamala
Apolisi oyenda usiku ndi omwe anatenga maliro ndi wina ovulalayo ndikupita nawo kuchipatala koma njingazo zatengedwa ndi apolisi.
Amene akuwa dziwa anthu chonde apite kuchipatala ku central.
Ngoziyi yachitika usiku angakhale kuti boma linaletsa anjinga za Moto kuyenda usiku.
DR MWALE