Sugar wakwera Mtengo

Sitolo zina zayamba kugulitsa paketi la shuga wa Illovo wolemera kilogilamu imodzi pamtengo wa K3,500. Izi ndi malinga ndi zomwe Avant Publications yapeza chakumasanaku m’boma la Thyolo.

Mtengowu ndi wokwera ndi K800 poyerekeza ndi momwe shuga amagulitsidwira sabata latha pomwe anali pamtengo wa K2,700 m’bomali.

Malingana ndi ogulitsa Malonda m’bomali ati belo la shuga layamba kugulitsidwa pa K58,000 kuchoka pa K45,000 mtengo umene beloli limagulitsidwira masiku angapo apitawa.

Kukwera Kwa shuga wa Illovo yomwe ndi kampane yaikulu yopanga shuga mdziko muno kukudza kamba kakusowa kwashugayu pamsika zomwe zikudetsa nkhawa anthu ambiri ogula shugayu.

(Dumisani Mwambazi-Mchinji)

avantmalawi.com

07/03/2024

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *