Kwabuka mpungwe pungwe kunyumba ya malamulo pomwe sipikala wa nyumba ya malamulo anauza mtsogoleri wa zipani zotsutsa m’nyumbayi kuti ayankhepo pa zimene nyumba ya malamulo yakambilana.
Pamenepa mayi Mary Navicha anaimilira kuti ayambe kuyankha kenako a Kondwani Nankhumwa nawo anaimanso kuti ayankhule. Apa panali kukokana kokana ndipo nyumba yonse inali phokoso lokhaloka.
kamba ka phokosoli sipikala wa nyumbayi analamula a Ben Phiri kuti atuluke m’nyumbayi kamba kosasunga mwambo.
Aphungu a Dpp akufuna mayi Mary Mavicha alankhule koma sipikala wakaniza a navicha kamba koti iwo akudziwa a Nankhumwa kuti ndiwo ali mtsogoleri wotsutsa m’nyumbayi.
Pakadali pano sipikala waimitsa zotsatilazi ndipo iye watuluka mnyumbayi. Ndipo abweranso pakata mphindi khumi
Nkhani yavuta ndi yoti ma atsogoleri azipani zotsutsa awiri onse akufuna kulankhula mnyumbayi.
Avant publications.
DR MWALE