Thupi la Malemu oyimba nyimbo za chikunja a katerere Ching’oma liyikidwa mmawa m’boma la Nsanje.
Tsogoleri wopuma wadziko lino a Joyce Banda ati ndi okhudzika kwambiri ndi imfa ya oyimbayu popeza Nyimbo za malemuyu zimapereka chilimbikitso ku miyoyo ya anthu ambiri Mdziko muno.

“Palibe tsiku ndi limodzi lomwe tinakhalako ndi zochitika osasewera nyimbo ya Ndili Nawo Mwayi,” watero Banda polemba pa tsamba lake la mchenzo la Facebook.
Komabe, Banda wati alephera kukhala nawo pa mwambo wa maliro a kastwiriyu popeza ali kunja kwa dziko lino.
“Ndikupemphera kuti amayi anzanga a JBF Mwai akandiyimilira ku mwambo wa maliro,” watero Banda.

Oyimba osiyanasiyana komanso anthu amene amatsatira nyimbo za malemu Katelele Ching’oma anakhamukira ku nyumba ya chisoni ya chipatala cha Kamuzu Central kumene kunali mwambo otenga thupi la malemuwa kupita nalo kwawo ku Msanje.
Katelele Ching’oma wamwalira m’banda kucha walero atadwa ma kanthawi kochepa.
Avant Publications